4 Iye sadzapitiriza kupatsa Yehova nsembe zavinyo.+ Mulungu sadzakondwera ndi nsembe zake,+ chifukwa zili ngati chakudya cha pamaliro.+ Onse amene adzadya chakudyacho adzadziipitsa. Chakudya chawo chidzakhala chongokhutitsa iwowo basi, ndipo sichidzalowa m’nyumba ya Yehova.+