Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • Levitiko 26:33
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 33 Ine ndidzakubalalitsani pakati pa anthu a mitundu ina,+ ndipo ndidzakusololerani lupanga ndi kukupitikitsani.+ Dziko lanu lidzakhala bwinja,+ ndipo mizinda yanu idzawonongedwa ndi kukhala mabwinja.

  • 2 Mafumu 24:14
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 14 Mfumuyo inatenga+ anthu onse a ku Yerusalemu, akalonga onse,+ amuna onse amphamvu ndi olimba mtima,+ mmisiri aliyense+ ndi munthu aliyense womanga makoma achitetezo, n’kupita nawo ku Babulo. Anthu onse amene inawatenga analipo 10,000. Palibe amene anatsala, kupatulapo anthu onyozeka+ okha a m’dzikolo.

  • 2 Mafumu 25:21
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 21 Mfumu ya Babuloyo inapha anthuwo+ ku Ribila m’dziko la Hamati.+ Choncho Ayuda anachoka kudziko lawo n’kupita ku ukapolo.+

  • Yeremiya 39:9
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 9 Nebuzaradani+ mkulu wa asilikali olondera mfumu,+ anatenga anthu ena onse otsala mumzindamo, anthu amene anathawira kwa mfumu ya Babulo ndi anthu ena onse amene anapulumuka kupita nawo ku ukapolo ku Babulo.+

  • Yeremiya 52:27
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 27 Mfumu ya Babulo inapha anthu amenewa+ ku Ribila+ m’dziko la Hamati.+ Choncho Ayuda anachoka kudziko lawo n’kupita ku ukapolo.+

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena