Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • Levitiko 26:33
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 33 Ine ndidzakubalalitsani pakati pa anthu a mitundu ina,+ ndipo ndidzakusololerani lupanga ndi kukupitikitsani.+ Dziko lanu lidzakhala bwinja,+ ndipo mizinda yanu idzawonongedwa ndi kukhala mabwinja.

  • Deuteronomo 4:26
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 26 ndikutenga kumwamba ndi dziko lapansi+ lero monga mboni zokutsutsani, kuti mudzafafanizidwa mwamsanga m’dziko limene mukupita kukalitenga mutawoloka Yorodano. Simudzatalikitsa masiku anu m’dzikomo chifukwa mudzawonongedwa ndithu.+

  • Deuteronomo 28:36
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 36 Yehova adzakuyendetsa+ pamodzi ndi mfumu+ yako imene udzadziikira, kukupititsa ku mtundu umene iweyo kapena makolo ako simunaudziwe. Kumeneko udzatumikira milungu ina, yamtengo kapena yamwala.+

  • Deuteronomo 28:64
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 64 “Yehova adzakumwazani mwa anthu a mitundu yonse kuchokera kumalekezero ena a dziko mpaka kumalekezero enanso a dziko.+ Kumeneko mukatumikira milungu ina imene inuyo kapena makolo anu simunaidziwe, milungu yamtengo ndi milungu yamwala.+

  • 2 Mafumu 23:27
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 27 Koma Yehova anati: “Yuda+ nayenso ndim’chotsa pamaso panga+ monga mmene ndinachotsera Isiraeli,+ ndipo ndithu ndidzakana ngakhale mzinda wa Yerusalemu umene ndinausankha, ndi nyumba imene ndinanena kuti, ‘Dzina langa lizikhala pamenepo.’”+

  • Yeremiya 24:9
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 9 Ndidzawasandutsa chinthu chimene maufumu onse a padziko lapansi adzanthunthumira nacho, chifukwa cha masoka aakulu amene ndidzawagwetsera.+ Anthu a mitundu ina adzawatonza, kuwayesa chosereula, kuwanyoza+ ndipo adzakhala otembereredwa+ kulikonse kumene ndidzawabalalitsirako.+

  • Yeremiya 25:11
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 11 Dziko lonseli lidzakhala bwinja, chinthu chodabwitsa, ndipo mitundu imeneyi idzatumikira mfumu ya ku Babulo zaka 70.”’+

  • Ezekieli 12:25
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 25 ‘“Pakuti ine Yehova ndidzalankhula, ndipo mawu amene ndidzalankhulewo adzakwaniritsidwadi.+ Sindidzazengerezanso+ chifukwa ine ndidzalankhula mawu m’masiku anu,+ inu a m’nyumba yopanduka, ndipo mawuwo ndidzawakwaniritsa,” watero Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa.’”

  • Ezekieli 24:14
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 14 Tsoka lako lidzabwera ndithu+ ndipo ndidzachitapo kanthu. Sindidzazengereza,+ kumva chisoni+ kapena kusintha maganizo.+ Iwo adzakuweruza mogwirizana ndi njira zako ndi zochita zako.+ Ine Yehova ndanena,’+ watero Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa.”

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena