Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • Yesaya 14:24
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 24 Yehova wa makamu walumbira+ kuti: “Ndithu zimene ndaganiza zidzachitika, ndipo zimene ndakonza sizidzalephereka.+

  • Yesaya 55:11
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 11 ndi mmenenso adzakhalire mawu otuluka pakamwa panga.+ Sadzabwerera kwa ine popanda kukwaniritsa cholinga chake,+ koma adzachitadi zimene ine ndikufuna+ ndipo adzakwaniritsadi zimene ndinawatumizira.+

  • Maliro 2:17
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 17 Yehova wachita zimene anali kuganiza.+ Wakwaniritsa zimene ananena,+

      Zimene analamula kalekale.+ Wapasula zinthu ndipo sanamve chisoni.+

      Wachititsa adani ako kusangalala+ chifukwa cha zimene zakuchitikira. Wakweza nyanga ya adani+ ako.

  • Danieli 9:12
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 12 Inu munachitadi zimene munachenjeza kuti mudzatichitira,+ ifeyo ndi atsogoleri athu.+ Munatigwetsera tsoka lalikulu ndipo tsoka limene lagwera Yerusalemu silinachitikeponso padziko lonse lapansi.+

  • Zekariya 1:6
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 6 Kodi zimene ndinalamula atumiki anga aneneri+ m’mawu anga ndi m’malangizo anga, sizinawachitikire makolo anu?’+ Chotero iwo anabwerera kwa ine ndi kunena kuti: ‘Yehova wa makamu watichitira zimene anakonza kuti atichitire+ mogwirizana ndi njira zathu ndi zochita zathu.’”+

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena