Salimo 137:3 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 3 Kumeneko, amene anatigwira ukapolo anatiuza kuti tiwaimbire nyimbo,+Ndipo otinyozawo anatipempha kuti tiwasangalatse.+ Iwo anati:“Tiimbireni imodzi mwa nyimbo za ku Ziyoni.”+ Miyambo 24:17 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 17 Mdani wako akagwa usamasangalale ndipo akapunthwa, mtima wako usamakondwere,+ Maliro 2:16 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 16 Adani ako onse akukutsegulira pakamwa.+Akuimba mluzu ndi kukukukutira mano.+ Iwo akunena kuti: “Ameneyu timumeza.+Ndithu, lero ndi tsiku limene takhala tikuyembekezera.+ Lafikadi! Taliona!”+
3 Kumeneko, amene anatigwira ukapolo anatiuza kuti tiwaimbire nyimbo,+Ndipo otinyozawo anatipempha kuti tiwasangalatse.+ Iwo anati:“Tiimbireni imodzi mwa nyimbo za ku Ziyoni.”+
16 Adani ako onse akukutsegulira pakamwa.+Akuimba mluzu ndi kukukukutira mano.+ Iwo akunena kuti: “Ameneyu timumeza.+Ndithu, lero ndi tsiku limene takhala tikuyembekezera.+ Lafikadi! Taliona!”+