13 “Yambani kumweta ndi chikwakwa,+ pakuti zokolola zacha.+ Bwerani, tsikirani kuno, pakuti moponderamo mphesa mwadzaza.+ Malo ogweramo vinyo wake asefukira, pakuti zoipa za anthu a mitundu ina zachuluka kwambiri.+
19 Mngeloyo+ anatsitsira chikwakwa chake kudziko lapansi mwamphamvu, ndi kumweta mpesa+ wa padziko lapansi. Ndiyeno anauponya m’choponderamo mphesa chachikulu cha mkwiyo wa Mulungu.+