Yesaya 17:10 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 10 Popeza waiwala+ Mulungu wa chipulumutso chako,+ ndipo Thanthwe+ la chitetezo chako sunalikumbukire, n’chifukwa chake ukulima minda yokongola n’kumabzalamo mphukira ya mlendo. Yeremiya 2:32 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 32 Kodi namwali angaiwale zodzikongoletsera? Kodi mkwatibwi angaiwale lamba wake wa pachifuwa? Koma anthu anga andiiwala kwa masiku osawerengeka.+ Yeremiya 3:21 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 21 Panjira zodutsidwadutsidwa pamveka mawu a ana a Isiraeli, kulira ndi kuchonderera kwawo. Pakuti iwo akhotetsa njira zawo+ ndipo aiwala Yehova Mulungu wawo.+ Yeremiya 13:25 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 25 Limeneli ndilo gawo lako, malo ako amene ndakuyezera,”+ watero Yehova, “chifukwa chakuti wandiiwala+ ndipo ukupitirizabe kukhulupirira zinthu zachinyengo.+
10 Popeza waiwala+ Mulungu wa chipulumutso chako,+ ndipo Thanthwe+ la chitetezo chako sunalikumbukire, n’chifukwa chake ukulima minda yokongola n’kumabzalamo mphukira ya mlendo.
32 Kodi namwali angaiwale zodzikongoletsera? Kodi mkwatibwi angaiwale lamba wake wa pachifuwa? Koma anthu anga andiiwala kwa masiku osawerengeka.+
21 Panjira zodutsidwadutsidwa pamveka mawu a ana a Isiraeli, kulira ndi kuchonderera kwawo. Pakuti iwo akhotetsa njira zawo+ ndipo aiwala Yehova Mulungu wawo.+
25 Limeneli ndilo gawo lako, malo ako amene ndakuyezera,”+ watero Yehova, “chifukwa chakuti wandiiwala+ ndipo ukupitirizabe kukhulupirira zinthu zachinyengo.+