Miyambo 17:5 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 5 Wonyoza munthu wosauka amanyoza amene anam’panga.+ Amene amasangalala ndi tsoka la wina sadzalephera kulangidwa.+ Miyambo 24:17 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 17 Mdani wako akagwa usamasangalale ndipo akapunthwa, mtima wako usamakondwere,+ Ezekieli 26:2 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 2 “Iwe mwana wa munthu, Turo+ wanena Yerusalemu+ kuti, ‘Eyaa! Zakhala bwino! Mzindawo wathyoledwa.+ Mzinda umene unali kukopa anthu a mitundu ina+ wathyoledwa. Tsopano ine zinthu zindiyendera bwino. Ndilemera chifukwa mzindawo wawonongedwa.’+ Ezekieli 35:2 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 2 “Iwe mwana wa munthu, yang’ana+ kudera lamapiri la Seiri+ ndipo ulosere zoipa zimene zidzachitikire deralo.+ Ezekieli 35:12 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 12 Iwe udzadziwa kuti ine Yehova, ndinamva mawu onse achipongwe amene unanenera mapiri a ku Isiraeli.+ Pakuti iwe unanena kuti: “Mapiri aja awonongedwa. Aperekedwa kwa ife kuti akhale chakudya chathu.”+
5 Wonyoza munthu wosauka amanyoza amene anam’panga.+ Amene amasangalala ndi tsoka la wina sadzalephera kulangidwa.+
2 “Iwe mwana wa munthu, Turo+ wanena Yerusalemu+ kuti, ‘Eyaa! Zakhala bwino! Mzindawo wathyoledwa.+ Mzinda umene unali kukopa anthu a mitundu ina+ wathyoledwa. Tsopano ine zinthu zindiyendera bwino. Ndilemera chifukwa mzindawo wawonongedwa.’+
2 “Iwe mwana wa munthu, yang’ana+ kudera lamapiri la Seiri+ ndipo ulosere zoipa zimene zidzachitikire deralo.+
12 Iwe udzadziwa kuti ine Yehova, ndinamva mawu onse achipongwe amene unanenera mapiri a ku Isiraeli.+ Pakuti iwe unanena kuti: “Mapiri aja awonongedwa. Aperekedwa kwa ife kuti akhale chakudya chathu.”+