-
Ezekieli 36:5Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
5 Mawu amene Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa, wanena ndi akuti, ‘Ndithudi, ndidzadzudzula anthu otsala a mitundu ina ndiponso Edomu yense nditakwiya kwambiri.+ Ndidzadzudzula amene anatenga dziko langa kuti likhale lawo. Iwo analitenga akusangalala+ komanso kunyoza mumtima mwawo+ poona kuti atenga dzikolo ndi malo ake odyetserako ziweto.’”’+
-
-
Amosi 1:11Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
11 “Yehova wanena kuti, ‘Chifukwa chakuti Edomu wandipandukira mobwerezabwereza,+ sindidzamusinthira chigamulo changa. Sindidzamusinthira chigamulocho chifukwa chakuti anathamangitsa m’bale wake ndi lupanga,+ sanasonyeze chifundo,+ akupitiriza kukhadzulakhadzula zinthu ali wokwiya komanso akukhalabe wokwiya mosalekeza.+
-