-
Salimo 83:5Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
5 Pakuti ndi mtima wonse, iwo amagawana nzeru,+
Ndipo anapangana pangano lotsutsana ndi inu.+
-
Amosi 1:11Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
11 “Yehova wanena kuti, ‘Chifukwa chakuti Edomu wandipandukira mobwerezabwereza,+ sindidzamusinthira chigamulo changa. Sindidzamusinthira chigamulocho chifukwa chakuti anathamangitsa m’bale wake ndi lupanga,+ sanasonyeze chifundo,+ akupitiriza kukhadzulakhadzula zinthu ali wokwiya komanso akukhalabe wokwiya mosalekeza.+
-
-
-