Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • Salimo 137:7
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    •  7 Inu Yehova, kumbukirani+ zimene ana a Edomu+ ananena pa tsiku limene Yerusalemu anawonongedwa,+

      Iwo anati: “Fafanizani mzindawo! Ufafanizeni mpaka pamaziko ake!”+

  • Yesaya 34:5
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 5 “Pakuti lupanga langa+ lidzakhala magazi okhaokha kumwambako. Lupangalo lidzatsikira pa Edomu+ ndi pa anthu amene ndikufuna kuwawononga+ mogwirizana ndi chilungamo changa.

  • Ezekieli 25:13
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 13 Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa, wanena kuti: “Ine ndidzatambasulira Edomu+ dzanja langa ndi kupha anthu ndi ziweto m’dzikolo.+ Ndidzalisandutsa bwinja kuyambira ku Temani+ mpaka ku Dedani.+ Iwo adzaphedwa ndi lupanga.

  • Ezekieli 35:15
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 15 Pakuti unali kusangalala chifukwa chakuti cholowa cha nyumba ya Isiraeli chinawonongedwa, ine ndidzachitanso chimodzimodzi kwa iwe.+ Iwe dera lamapiri la Seiri ndiponso Edomu yense, mudzasanduka bwinja,+ ndipo anthu adzadziwa kuti ine ndine Yehova.’”+

  • Amosi 1:11
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 11 “Yehova wanena kuti, ‘Chifukwa chakuti Edomu wandipandukira mobwerezabwereza,+ sindidzamusinthira chigamulo changa. Sindidzamusinthira chigamulocho chifukwa chakuti anathamangitsa m’bale wake ndi lupanga,+ sanasonyeze chifundo,+ akupitiriza kukhadzulakhadzula zinthu ali wokwiya komanso akukhalabe wokwiya mosalekeza.+

  • Obadiya 13
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 13 Iwe sunayenera kulowa pachipata cha anthu anga pa tsiku limene anakumana ndi tsoka.+ Ndithu iweyo sunayenera kuyang’anitsitsa tsoka la m’bale wako pa tsiku limene anawonongedwa. Ndipo sunayeneranso kutambasula dzanja lako ndi kutenga chuma chake pa tsiku limene iye anakumana ndi tsoka.+

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena