2 Mbiri 36:21 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 21 Zimenezi zinachitika pokwaniritsa mawu a Yehova amene ananena kudzera mwa Yeremiya,+ mpaka pamene dzikolo linalipira masabata ake.+ Masiku onse amene dzikolo linali bwinja linali kusunga sabata mpaka linakwaniritsa zaka 70.+ Yesaya 6:11 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 11 Pamenepo ndinafunsa kuti: “Mpaka liti, Yehova?”+ Iye anayankha kuti: “Mpaka mizinda yawo itawonongedwa n’kukhala bwinja, yopanda wokhalamo. Mpaka nyumba zawo zitakhala zopanda anthu okhalamo, ndiponso mpaka nthaka itawonongekeratu.+ Yeremiya 9:11 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 11 Yerusalemu ndidzamusandutsa milu ya miyala+ ndiponso malo obisalamo mimbulu.+ Mizinda ya Yuda ndidzaisandutsa mabwinja, malo opanda wokhalamo.+ Yeremiya 44:2 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 2 “Yehova wa makamu, Mulungu wa Isiraeli wanena kuti, ‘Inu mwaona masoka onse amene ndagwetsera Yerusalemu+ ndi mizinda yonse ya Yuda. Lero mizinda imeneyi yakhala mabwinja ndipo palibe amene akukhalamo.+ Ezekieli 36:34 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 34 Anthu adzalima m’dziko limene linali lowonongedwa. Adzalima m’dziko limene aliyense wodutsa ankaliona kuti ndi bwinja.+ Mika 7:13 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 13 Dzikoli lidzakhala bwinja chifukwa cha zochita za anthu okhala mmenemo ndi zotsatirapo za zochita zawozo.+
21 Zimenezi zinachitika pokwaniritsa mawu a Yehova amene ananena kudzera mwa Yeremiya,+ mpaka pamene dzikolo linalipira masabata ake.+ Masiku onse amene dzikolo linali bwinja linali kusunga sabata mpaka linakwaniritsa zaka 70.+
11 Pamenepo ndinafunsa kuti: “Mpaka liti, Yehova?”+ Iye anayankha kuti: “Mpaka mizinda yawo itawonongedwa n’kukhala bwinja, yopanda wokhalamo. Mpaka nyumba zawo zitakhala zopanda anthu okhalamo, ndiponso mpaka nthaka itawonongekeratu.+
11 Yerusalemu ndidzamusandutsa milu ya miyala+ ndiponso malo obisalamo mimbulu.+ Mizinda ya Yuda ndidzaisandutsa mabwinja, malo opanda wokhalamo.+
2 “Yehova wa makamu, Mulungu wa Isiraeli wanena kuti, ‘Inu mwaona masoka onse amene ndagwetsera Yerusalemu+ ndi mizinda yonse ya Yuda. Lero mizinda imeneyi yakhala mabwinja ndipo palibe amene akukhalamo.+
34 Anthu adzalima m’dziko limene linali lowonongedwa. Adzalima m’dziko limene aliyense wodutsa ankaliona kuti ndi bwinja.+
13 Dzikoli lidzakhala bwinja chifukwa cha zochita za anthu okhala mmenemo ndi zotsatirapo za zochita zawozo.+