2 “Lamula ana a Isiraeli kuti pacholowa chawo cha malo, akapatseko Alevi mizinda+ yokhalamo. Akaperekenso kwa Aleviwo malo onse odyetserako ziweto ozungulira mizindayo.+
4 Malo oyerawa adzakhale gawo la ansembe m’dzikoli.+ Ansembewo ndi atumiki a pamalo opatulika ndipo amayandikira kwa Yehova ndi kumutumikira.+ Malo amenewa adzakhale awo kuti adzamangepo nyumba zawo. Adzakhalenso malo opatulika omangapo nyumba yopatulika.