7 Utembereredwe mkwiyo wawo+ chifukwa ndi wankhanza,+ ndi ukali wawo chifukwa umachita mwachiwawa.+ Ndidzawamwaza mwa Yakobo, ndipo ndidzawabalalitsa mwa Isiraeli.+
4 Ana a Yosefe anakhala mafuko awiri,+ la Manase+ ndi la Efuraimu.+ Iwowa anapatsa Alevi mizinda+ yoti azikhalamo, malo odyetserako ziweto, ndi osungirako katundu wawo, koma sanawagawire cholowa cha malo.+