13 Elisa anafunsa mfumu ya Isiraeli kuti: “Ndili nanu chiyani?+ Pitani kwa aneneri+ a bambo anu ndi kwa aneneri a mayi anu.” Koma mfumu ya Isiraeliyo inati: “Ayi musatero, chifukwa Yehova wasonkhanitsa ife mafumu atatu kuti atipereke m’manja mwa Mowabu.”+