Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • Yesaya 5:24
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 24 Chotero monga momwe lawi la moto limanyeketsera mapesi+ komanso monga mmene udzu wouma umanyekera m’malawi a moto, muzu wawo udzawola n’kuyamba kununkha.+ Maluwa awo adzauma n’kuuluzika ngati fumbi, chifukwa akana malamulo a Yehova wa makamu+ ndipo anyoza mawu a Woyera wa Isiraeli.+

  • Yeremiya 4:7
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 7 Wowonongayo akubwera ngati mkango umene ukutuluka paziyangoyango pamene umakhala.+ Amene akuwononga mitundu ya anthu wanyamuka.+ Wachoka m’malo ake kuti adzasandutse dziko lanu chinthu chodabwitsa. Mizinda yanu idzagwa ndi kukhala mabwinja moti sipadzapezeka wokhalamo.+

  • Yeremiya 7:20
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 20 Choncho Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa, wanena kuti, ‘Taonani! Mkwiyo wanga ndi ukali wanga zikutsanulidwa pamalo awa,+ pamunthu, pachiweto, pamtengo wakuthengo,+ ndi pachipatso chilichonse chochokera m’nthaka yawo, ndipo udzayaka moti sudzazimitsidwa.’+

  • Ezekieli 20:47
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 47 Uuze nkhalango ya kum’mwerayo kuti, ‘Imva mawu a Yehova. Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa, wanena kuti: “Ine ndikukuyatsa moto.+ Motowo unyeketsa mtengo uliwonse wauwisi ndi mtengo uliwonse wouma.+ Malawi a motowo sadzatheka kuwazimitsa,+ ndipo nkhope zonse,* kuchokera kum’mwera mpaka kumpoto zidzapsa ndi moto.+

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena