Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • Ekisodo 3:8
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 8 Choncho nditsikira kwa iwo kuti ndiwalanditse m’manja mwa Aiguputo,+ ndi kuwatulutsa m’dzikolo, n’kuwalowetsa m’dziko labwino komanso lalikulu, dziko loyenda mkaka ndi uchi.+ Ndiwalowetsa m’dziko la Akanani, Ahiti, Aamori, Aperizi, Ahivi, ndi Ayebusi.+

  • Deuteronomo 6:3
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 3 Ndipo inu Aisiraeli, muzimvetsera ndi kutsatira mfundo ndi malamulo ake mosamala,+ kuti zinthu zikuyendereni bwino,+ ndi kuti muchuluke kwambiri m’dziko loyenda mkaka ndi uchi, monga mmene Yehova Mulungu wa makolo anu anakulonjezerani.+

  • Deuteronomo 8:7
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 7 Pakuti Yehova Mulungu wanu akukulowetsani m’dziko labwino,+ dziko la zigwa* za madzi,+ akasupe ndi madzi ochuluka otuluka m’zigwa ndi m’madera a mapiri,

  • Yoswa 5:6
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 6 Ana a Isiraeliwo anayenda m’chipululu zaka 40,+ mpaka amuna onse otha kupita kunkhondo amene anatuluka mu Iguputo atatha, amene sanamvere mawu a Yehova. Amenewo Yehova anawalumbirira kuti sadzawalola kuona dziko+ limene Yehova analumbirira makolo awo kuti adzalipereka kwa anthu ake,*+ dziko loyenda mkaka ndi uchi.+

  • Yeremiya 11:5
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 5 kuti ndikwaniritse lumbiro limene ndinalumbirira makolo anu+ kuti ndidzawapatsa dziko loyenda mkaka ndi uchi,+ monga mmene zilili lero.’”’”

      Pamenepo ine ndinayankha kuti: “Zikhale momwemo,* inu Yehova.”

  • Yeremiya 32:22
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 22 “Patapita nthawi munawapatsa dziko lino, limene munalumbirira makolo awo kuti mudzawapatsa,+ dziko loyenda mkaka ndi uchi.+

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena