Yesaya 13:11 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 11 Nthaka ndidzaibwezera zoipa zake,+ ndipo anthu oipa ndidzawabwezera zolakwa zawo. Kunyada kwa anthu odzikuza ndidzakuthetsa, ndipo ndidzatsitsa olamulira ankhanza ndi odzikweza.+ Yeremiya 25:12 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 12 “‘Ndiyeno zaka 70 zimenezo zikadzakwanira,+ ndidzabwezera mfumu ya Babulo ndi mtundu umenewo zolakwa zawo.+ Ndidzabwezera zolakwa za dziko la Akasidi+ ndipo dziko lawolo lidzakhala mabwinja mpaka kalekale,’+ watero Yehova. Yeremiya 27:7 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 7 Choncho mitundu yonse ya anthu idzatumikira iyeyo,+ mwana wake wamwamuna ndi mdzukulu wake mpaka idzafike nthawi yoti ufumu wake uthe.+ Pamenepo, mitundu yambiri ya anthu ndi mafumu amphamvu adzamugwiritsa ntchito ngati wantchito wawo.’+ Yeremiya 50:1 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 50 Yehova ananena mawu okhudza Babulo,+ dziko la Akasidi,+ kudzera mwa mneneri Yeremiya. Iye anati: Yeremiya 51:11 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 11 “Nolani mivi yanu.+ Dzitetezeni ndi zishango zozungulira, amuna inu. Yehova wautsa mitima ya mafumu a Amedi,+ chifukwa akufuna kulanga Babulo ndi kumuwononga.+ Yehova akufuna kubwezera Babulo chilango chifukwa cha kachisi wake.+
11 Nthaka ndidzaibwezera zoipa zake,+ ndipo anthu oipa ndidzawabwezera zolakwa zawo. Kunyada kwa anthu odzikuza ndidzakuthetsa, ndipo ndidzatsitsa olamulira ankhanza ndi odzikweza.+
12 “‘Ndiyeno zaka 70 zimenezo zikadzakwanira,+ ndidzabwezera mfumu ya Babulo ndi mtundu umenewo zolakwa zawo.+ Ndidzabwezera zolakwa za dziko la Akasidi+ ndipo dziko lawolo lidzakhala mabwinja mpaka kalekale,’+ watero Yehova.
7 Choncho mitundu yonse ya anthu idzatumikira iyeyo,+ mwana wake wamwamuna ndi mdzukulu wake mpaka idzafike nthawi yoti ufumu wake uthe.+ Pamenepo, mitundu yambiri ya anthu ndi mafumu amphamvu adzamugwiritsa ntchito ngati wantchito wawo.’+
11 “Nolani mivi yanu.+ Dzitetezeni ndi zishango zozungulira, amuna inu. Yehova wautsa mitima ya mafumu a Amedi,+ chifukwa akufuna kulanga Babulo ndi kumuwononga.+ Yehova akufuna kubwezera Babulo chilango chifukwa cha kachisi wake.+