Levitiko 26:26 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 26 Ndikadzathyola ndodo zanu zopachikapo mkate wozungulira woboola pakati,+ akazi 10 adzaphika mkate mu uvuni umodzi, ndipo adzakugawirani mochita kukuyezerani pamuyezo.+ Chotero mudzadya koma simudzakhuta.+ Mika 6:14 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 14 Inuyo mudzadya koma simudzakhuta ndipo mudzamvabe njala.+ Mudzanyamula zinthu kuti mukazisunge pabwino koma simudzatha kuziteteza. Zinthu zilizonse zimene mudzazitenge, ine ndidzazipereka kwa adani anu kuti aziwononge.+ Hagai 1:6 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 6 Mwafesa mbewu zambiri koma zokolola zanu n’zochepa.+ Mukudya koma simukukhuta.+ Mukumwa koma simukukhutira.* Mukuvala zovala koma simukumva kutentha. Amene akugwira ganyu akulandirira ndalama zake m’matumba obowoka.’”+
26 Ndikadzathyola ndodo zanu zopachikapo mkate wozungulira woboola pakati,+ akazi 10 adzaphika mkate mu uvuni umodzi, ndipo adzakugawirani mochita kukuyezerani pamuyezo.+ Chotero mudzadya koma simudzakhuta.+
14 Inuyo mudzadya koma simudzakhuta ndipo mudzamvabe njala.+ Mudzanyamula zinthu kuti mukazisunge pabwino koma simudzatha kuziteteza. Zinthu zilizonse zimene mudzazitenge, ine ndidzazipereka kwa adani anu kuti aziwononge.+
6 Mwafesa mbewu zambiri koma zokolola zanu n’zochepa.+ Mukudya koma simukukhuta.+ Mukumwa koma simukukhutira.* Mukuvala zovala koma simukumva kutentha. Amene akugwira ganyu akulandirira ndalama zake m’matumba obowoka.’”+