Yesaya 30:14 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 14 Munthu adzaugwetsa ngati mmene amaphwanyira mtsuko waukulu wadothi,+ mtsukowo n’kuphwanyikiratu wonse n’kungokhala tizidutswatizidutswa, ndipo patizidutswapo osapezeka ngakhale phale loti n’kupalira moto kapena kutungira madzi padambo.”+ Yeremiya 22:28 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 28 Kodi munthu uyu Koniya+ wangokhala chiwiya chonyozeka, chophwanyika+ komanso chosasangalatsa?+ N’chifukwa chiyani iyeyu ndi ana ake akuyenera kugwetsedwa ndi kuponyedwa kudziko limene sakulidziwa?’+ Yeremiya 48:38 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 38 “‘Anthu akulira pamadenga onse a nyumba za ku Mowabu ndi m’mabwalo ake onse.+ Akulira chifukwa ndaphwanya Mowabu ngati chiwiya chimene sichikundikondweretsa,’+ watero Yehova.
14 Munthu adzaugwetsa ngati mmene amaphwanyira mtsuko waukulu wadothi,+ mtsukowo n’kuphwanyikiratu wonse n’kungokhala tizidutswatizidutswa, ndipo patizidutswapo osapezeka ngakhale phale loti n’kupalira moto kapena kutungira madzi padambo.”+
28 Kodi munthu uyu Koniya+ wangokhala chiwiya chonyozeka, chophwanyika+ komanso chosasangalatsa?+ N’chifukwa chiyani iyeyu ndi ana ake akuyenera kugwetsedwa ndi kuponyedwa kudziko limene sakulidziwa?’+
38 “‘Anthu akulira pamadenga onse a nyumba za ku Mowabu ndi m’mabwalo ake onse.+ Akulira chifukwa ndaphwanya Mowabu ngati chiwiya chimene sichikundikondweretsa,’+ watero Yehova.