Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • Ekisodo 32:4
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 4 Pamenepo iye analandira golideyo kuchokera kwa anthuwo ndipo pogwiritsa ntchito chosemera, anam’panga+ kukhala fano la mwana wa ng’ombe+ lopangidwa ndi golide wosungunula. Zitatero iwo anayamba kunena kuti: “Uyu ndiye Mulungu wanu, Aisiraeli inu, amene anakutulutsani m’dziko la Iguputo.”+

  • Oweruza 17:4
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 4 Koma Mika anabweza ndalamazo kwa mayi ake, ndipo mayi akewo anatenga ndalama zasiliva zokwana 200 n’kuzipereka kwa wosula siliva.+ Pamenepo wosula silivayo anapanga chifaniziro chosema+ ndi chifaniziro chopangidwa ndi chitsulo chosungunula.+ Zinthu zimenezi anaziika m’nyumba ya Mika.

  • Yesaya 46:6
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 6 Pali anthu amene amakhuthula golide m’zikwama, ndi kuyeza siliva pasikelo. Iwo amalemba ganyu mmisiri wa zitsulo ndipo iye amapanga mulungu ndi zinthu zimenezi.+ Kenako anthuwo amayamba kuweramira ndi kugwadira mulunguyo.+

  • Hoseya 8:4
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 4 Iwo aika mafumu,+ koma osati mwa kufuna kwanga. Aika akalonga, popanda ine kuvomereza. Adzipangira mafano+ pogwiritsa ntchito siliva ndi golide wawo ndipo zimenezi zidzawawonongetsa.+

  • Hoseya 13:2
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 2 Tsopano anthu ake akuchita machimo ena ndipo akugwiritsa ntchito siliva wawo popanga zifanizo zachitsulo chosungunula.+ Zifanizo zimenezo ndi mafano opangidwa mogwirizana ndi maganizo awo,+ koma zonsezi ndi ntchito za amisiri.+ Iwo amauza mafanowo kuti, ‘Amuna opereka nsembe apsompsone mafano a ana ang’ombe.’+

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena