Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • Yesaya 11:12
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 12 Iye adzakwezera chizindikiro mitundu ya anthu n’kusonkhanitsa Aisiraeli omwe anamwazikana.+ Ndipo adzasonkhanitsa pamodzi Ayuda omwe anabalalika, kuchokera kumalekezero anayi a dziko lapansi.+

  • Yesaya 43:5
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 5 “Usachite mantha chifukwa ine ndili nawe.+ Ndidzabweretsa mbewu yako kuchokera kotulukira dzuwa, ndipo ndidzakusonkhanitsani pamodzi kuchokera kolowera dzuwa.+

  • Yesaya 49:12
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 12 Taonani! Awa adzachokera kutali,+ ndipo awa adzachokera kumpoto+ ndi kumadzulo.+ Awanso adzachokera kudziko la Sinimu.”

  • Yeremiya 23:8
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 8 Koma adzalumbira kuti, ‘Pali Yehova Mulungu wamoyo amene anatulutsa a m’nyumba ya Isiraeli ndi kuwabweretsa kuno kuchokera m’dziko la kumpoto komanso kuchokera m’mayiko onse kumene ndinawabalalitsira’ ndipo adzakhala m’dziko lawo.”+

  • Ezekieli 34:12
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 12 Ndidzasamalira nkhosa zanga ngati mmene amachitira munthu amene amadyetsa gulu la nkhosa+ zake pamene ali pakati pa nkhosa zimene zinabalalika.+ Pa tsiku la mitambo ndi mdima wandiweyani, ndidzapulumutsa nkhosazo kuchokera m’malo onse kumene zinabalalikira.+

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena