9 Ndiyeno m’chaka chachisanu cha ulamuliro wa Yehoyakimu+ mwana wa Yosiya, mfumu ya Yuda, m’mwezi wa 9,+ analengeza kuti anthu onse a mu Yerusalemu ndi anthu onse amene anali kubwera ku Yerusalemu kuchokera m’mizinda ya Yuda asale kudya pamaso pa Yehova.+