Ekisodo 10:22 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 22 Nthawi yomweyo, Mose anatambasula dzanja lake ndi kuloza kumwamba, ndipo m’dziko lonse la Iguputo munachita mdima wandiweyani kwa masiku atatu.+ Ekisodo 14:20 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 20 Mtambowo unaima pakati pa Aiguputo ndi Aisiraeli.+ Mbali imodzi unali kuchititsa mdima, ndipo mbali ina unali kuwaunikira usiku.+ Ndipo gulu la Aiguputo silinayandikire gulu la Aisiraeli usiku wonse. Yesaya 5:30 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 30 Iwo adzabangulira nyamayo m’tsiku limenelo ngati mkokomo wa nyanja.+ Munthu adzayang’ana dzikolo n’kuona kuti muli mdima womvetsa chisoni.+ Ngakhale kuwala kudzasanduka mdima chifukwa cha mvula imene idzagwe m’dzikolo. Yeremiya 13:16 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 16 Patsani Yehova Mulungu wanu ulemerero+ asanachititse mdima,+ komanso mapazi anu asanapunthwe pamapiri madzulo dzuwa litalowa.+ Mudzayembekeza kuwala+ koma iye adzabweretsa mdima,+ ndipo adzachititsa mdima wandiweyani.+ Amosi 8:9 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 9 “Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa, wanena kuti, ‘Pa tsiku limenelo ndidzachititsa kuti dzuwa lilowe masanasana,+ ndiponso kuti m’dziko mugwe mdima dzuwa lisanalowe.
22 Nthawi yomweyo, Mose anatambasula dzanja lake ndi kuloza kumwamba, ndipo m’dziko lonse la Iguputo munachita mdima wandiweyani kwa masiku atatu.+
20 Mtambowo unaima pakati pa Aiguputo ndi Aisiraeli.+ Mbali imodzi unali kuchititsa mdima, ndipo mbali ina unali kuwaunikira usiku.+ Ndipo gulu la Aiguputo silinayandikire gulu la Aisiraeli usiku wonse.
30 Iwo adzabangulira nyamayo m’tsiku limenelo ngati mkokomo wa nyanja.+ Munthu adzayang’ana dzikolo n’kuona kuti muli mdima womvetsa chisoni.+ Ngakhale kuwala kudzasanduka mdima chifukwa cha mvula imene idzagwe m’dzikolo.
16 Patsani Yehova Mulungu wanu ulemerero+ asanachititse mdima,+ komanso mapazi anu asanapunthwe pamapiri madzulo dzuwa litalowa.+ Mudzayembekeza kuwala+ koma iye adzabweretsa mdima,+ ndipo adzachititsa mdima wandiweyani.+
9 “Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa, wanena kuti, ‘Pa tsiku limenelo ndidzachititsa kuti dzuwa lilowe masanasana,+ ndiponso kuti m’dziko mugwe mdima dzuwa lisanalowe.