32 Ndiyeno aliyense woitana pa dzina la Yehova adzapulumuka,+ pakuti m’phiri la Ziyoni ndiponso mu Yerusalemu mudzakhala anthu opulumuka+ monga mmene Yehova ananenera. Amenewa ndi anthu amene Yehova akuwaitana.”+
17 Ndipo chinjokacho chinakwiya ndi mkazi uja,+ moti chinapita kukachita nkhondo ndi otsala a mbewu yake, amene amasunga malamulo a Mulungu, amenenso ali ndi ntchito yochitira umboni+ za Yesu.