6 M’chaka cha 9 cha Hoshiya, mfumu ya Asuri inalanda Samariya+ n’kutenga Aisiraeli kupita nawo ku Asuri.+ Mfumuyo inakaika Aisiraeliwo ku Hala+ ndi ku Habori pafupi ndi mtsinje wa Gozani,+ ndiponso m’mizinda ya Amedi.+
7 ‘Ena mwa ana ako ochokera mwa iwe, amene iweyo udzakhale bambo wawo, nawonso adzatengedwa+ ndipo adzakhala nduna za panyumba+ ya mfumu ya ku Babulo.’”+