Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • 1 Samueli 15:11
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 11 “Ndikumva chisoni+ kuti ndinaika Sauli kukhala mfumu. Iye watembenuka,+ wasiya kunditsatira, ndipo sakumvera mawu anga.”+ Samueli anavutika maganizo kwambiri ndi nkhani imeneyi+ moti anafuulira Yehova usiku wonse.+

  • Yesaya 1:4
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 4 Tsoka kwa mtundu wochimwa,+ anthu olemedwa ndi zolakwa, mbewu yochita zoipa,+ ana obweretsa chiwonongeko.+ Iwo amusiya Yehova.+ Achitira Woyera wa Isiraeli zinthu zopanda ulemu,+ ndipo abwerera m’mbuyo.+

  • Yesaya 9:17
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 17 N’chifukwa chake Yehova sadzasangalalira ngakhale anyamata awo,+ ndipo sadzamvera chisoni ana awo amasiye* ndi akazi awo amasiye, pakuti onsewo ndi opanduka+ ndi ochita zoipa ndipo pakamwa paliponse pakulankhula zopanda nzeru. Chifukwa cha zonsezi, mkwiyo wake sunabwerere, ndipo dzanja lake lidakali lotambasula.+

  • Yeremiya 2:13
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 13 ‘chifukwa pali zinthu ziwiri zoipa zimene anthu anga achita: Iwo asiya ine+ kasupe wa madzi amoyo,+ ndipo akumba zitsime zawozawo, zitsime zong’ambika zimene sizingasunge madzi.’

  • Aheberi 3:12
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 12 Chenjerani abale, kuti pakati panu, wina asachoke kwa Mulungu wamoyo n’kukhala ndi mtima woipa wopanda chikhulupiriro.+

  • Aheberi 10:38
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 38 “Koma wolungama wanga adzakhala ndi moyo mwa chikhulupiriro chake,”+ ndipo “ngati wabwerera m’mbuyo, ine sindikondwera naye.”+

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena