Genesis 26:12 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 12 Zitatero, Isaki anayamba kubzala mbewu m’dzikomo.+ M’chaka chimenechi anakolola zochuluka moti pa mbewu zimene anabzala, anakolola zochuluka kuwirikiza nthawi 100,+ popeza Yehova anali kum’dalitsa.+ Levitiko 26:4 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 4 ndidzakugwetserani mvula pa nthawi yake.+ Nthaka idzakupatsani chakudya,+ ndipo mitengo ya m’munda idzakupatsani zipatso zake.+ Salimo 128:2 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 2 Pakuti udzadya zipatso za ntchito ya manja ako.+Udzakhala wodala ndipo zinthu zidzakuyendera bwino.+ Miyambo 3:10 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 10 Ukatero nkhokwe zako zidzakhala zodzaza+ ndipo zoponderamo mphesa zako zidzasefukira ndi vinyo watsopano.+ Miyambo 10:22 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 22 Madalitso a Yehova ndi amene amalemeretsa,+ ndipo sawonjezerapo ululu.+ Zekariya 8:12 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 12 ‘M’dzikolo mudzakhala mbewu ya mtendere.+ Mpesa udzabala zipatso+ ndipo dziko lapansi lidzapereka zokolola zake.+ Kumwamba kudzagwetsa mame ake.+ Ndidzachititsa kuti anthu otsala+ mwa anthu awa adzalandire zinthu zonsezi.+ Mateyu 6:33 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 33 “Chotero pitirizani kufunafuna ufumu choyamba ndi chilungamo chake,+ ndipo zina zonsezi zidzawonjezedwa kwa inu.+
12 Zitatero, Isaki anayamba kubzala mbewu m’dzikomo.+ M’chaka chimenechi anakolola zochuluka moti pa mbewu zimene anabzala, anakolola zochuluka kuwirikiza nthawi 100,+ popeza Yehova anali kum’dalitsa.+
4 ndidzakugwetserani mvula pa nthawi yake.+ Nthaka idzakupatsani chakudya,+ ndipo mitengo ya m’munda idzakupatsani zipatso zake.+
2 Pakuti udzadya zipatso za ntchito ya manja ako.+Udzakhala wodala ndipo zinthu zidzakuyendera bwino.+
10 Ukatero nkhokwe zako zidzakhala zodzaza+ ndipo zoponderamo mphesa zako zidzasefukira ndi vinyo watsopano.+
12 ‘M’dzikolo mudzakhala mbewu ya mtendere.+ Mpesa udzabala zipatso+ ndipo dziko lapansi lidzapereka zokolola zake.+ Kumwamba kudzagwetsa mame ake.+ Ndidzachititsa kuti anthu otsala+ mwa anthu awa adzalandire zinthu zonsezi.+
33 “Chotero pitirizani kufunafuna ufumu choyamba ndi chilungamo chake,+ ndipo zina zonsezi zidzawonjezedwa kwa inu.+