14 Chotero, popeza tili ndi mkulu wa ansembe wapamwamba, Yesu Mwana wa Mulungu,+ amene anapita kumwamba,+ tiyeni tipitirize kulengeza chikhulupiriro chathu mwa iye.+
8Ndiye kunena za zinthu zimene tikukambiranazi, mfundo yaikulu ndi iyi: Tili ndi mkulu wa ansembe+ ngati ameneyu, ndipo iye wakhala pansi kumwamba, kudzanja lamanja la mpando wachifumu wa Wolemekezeka.+