Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • Ekisodo 32:11
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 11 Pamenepo Mose anakhazika pansi mtima wa Yehova Mulungu wake.+ Iye anati: “N’chifukwa chiyani, inu Yehova, mukufuna kuti mkwiyo wanu+ uyakire anthu anu, amene munawatulutsa m’dziko la Iguputo mwa mphamvu zazikulu ndiponso ndi dzanja lamphamvu?

  • 1 Samueli 13:12
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 12 ndinaganiza+ kuti, ‘Tsopano Afilisitiwa abwera ku Giligala kuno kudzamenyana nane, ndipo sindinakhazike pansi mtima wa Yehova kuti atikomere mtima.’ Choncho ndakakamizika+ kupereka nsembe yopsereza.”

  • 1 Mafumu 13:6
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 6 Tsopano mfumuyo inauza munthu wa Mulungu woonayo kuti: “Chonde! Khazikani pansi mtima wa Yehova Mulungu wanu. Mundipempherere kuti dzanja langa libwerere mwakale.”+ Choncho munthu wa Mulungu woona uja anakhazikadi pansi+ mtima wa Yehova, moti dzanja la mfumu linabwerera mwakale, n’kukhala ngati mmene linalili poyamba.+

  • Yeremiya 26:19
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 19 Kodi Hezekiya mfumu ya Yuda ndi anthu onse a mu Yuda anamupha? Kodi iye sanaope Yehova ndi kukhazika pansi mtima wa Yehova?+ Kodi atatero, Yehova sanasinthe maganizo ake pa tsoka limene ananena kuti adzawagwetsera?+ Pamenepatu ife tikudziitanira tsoka lalikulu.+

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena