15 Ndidzaika+ chidani+ pakati pa iwe+ ndi mkaziyo,+ ndi pakati pa mbewu yako+ ndi mbewu yake.+ Mbewu ya mkaziyo+ idzaphwanya mutu wako,+ ndipo iwe+ udzaivulaza chidendene.”+
25 Inu ndinu ana+ a aneneri ndi a pangano limene Mulungu anapangana ndi makolo anu akale. Iye anauza Abulahamu kuti, ‘Kudzera mwa mbewu yako mabanja onse a padziko lapansi adzadalitsidwa.’+