Yesaya 44:18 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 18 Iwo sadziwa chilichonse+ ndipo samvetsetsa chilichonse+ chifukwa maso awo amatidwa kuti asamaone,+ ndipo mitima yawo ndi yosazindikira zinthu.+ Yeremiya 5:21 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 21 “Tsopano tamverani izi anthu opusa inu, anthu opanda nzeru mumtima mwanu,+ amene muli ndi maso koma simukuona,+ muli ndi makutu koma simukumva.+ Ezekieli 12:2 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 2 “Iwe mwana wa munthu, ukukhala pakati pa anthu opanduka+ omwe ali ndi maso koma saona,+ omwe ali ndi makutu koma samva,+ chifukwa ndi anthu opanduka.+ Mateyu 13:13 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 13 N’chifukwa chake ndikulankhula nawo mwa mafanizo. Pakuti ngakhale akuona, kuona kwawo n’kopanda phindu. Ngakhale akumva, kumva kwawo n’kopanda phindu, ndipo sazindikira tanthauzo lake.+
18 Iwo sadziwa chilichonse+ ndipo samvetsetsa chilichonse+ chifukwa maso awo amatidwa kuti asamaone,+ ndipo mitima yawo ndi yosazindikira zinthu.+
21 “Tsopano tamverani izi anthu opusa inu, anthu opanda nzeru mumtima mwanu,+ amene muli ndi maso koma simukuona,+ muli ndi makutu koma simukumva.+
2 “Iwe mwana wa munthu, ukukhala pakati pa anthu opanduka+ omwe ali ndi maso koma saona,+ omwe ali ndi makutu koma samva,+ chifukwa ndi anthu opanduka.+
13 N’chifukwa chake ndikulankhula nawo mwa mafanizo. Pakuti ngakhale akuona, kuona kwawo n’kopanda phindu. Ngakhale akumva, kumva kwawo n’kopanda phindu, ndipo sazindikira tanthauzo lake.+