Mateyu 6:20 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 20 Koma unjikani chuma chanu kumwamba,+ kumene njenjete kapena dzimbiri sizingawononge,+ ndiponso kumene mbala sizingathyole n’kuba. Mateyu 19:21 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 21 Yesu anamuuza kuti: “Ngati ukufuna kukhala wangwiro, pita kagulitse katundu wako ndipo ndalama zake upatse osauka. Ukatero udzakhala ndi chuma kumwamba,+ ndiyeno ubwere udzakhale wotsatira wanga.”+ Maliko 10:21 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 21 Yesu anamuyang’ana ndipo anam’konda. Kenako anamuuza kuti: “Chinthu chimodzi chikusowekabe mwa iwe: Pita kagulitse zilizonse zimene uli nazo ndipo ndalama zake upatse osauka. Ukatero udzakhala ndi chuma kumwamba, ndiyeno ubwere udzakhale wotsatira wanga.”+ Luka 12:33 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 33 Gulitsani+ zinthu zanu ndi kupereka mphatso zachifundo.+ Dzipangireni zikwama za ndalama zomwe sizingathe, kutanthauza chuma chosatha kumwamba,+ kumene mbala singafikeko, ndipo njenjete* singawononge. 1 Timoteyo 6:19 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 19 ndiponso asunge+ maziko abwino+ a tsogolo lawo monga chuma, kuti agwire mwamphamvu moyo weniweniwo.+
20 Koma unjikani chuma chanu kumwamba,+ kumene njenjete kapena dzimbiri sizingawononge,+ ndiponso kumene mbala sizingathyole n’kuba.
21 Yesu anamuuza kuti: “Ngati ukufuna kukhala wangwiro, pita kagulitse katundu wako ndipo ndalama zake upatse osauka. Ukatero udzakhala ndi chuma kumwamba,+ ndiyeno ubwere udzakhale wotsatira wanga.”+
21 Yesu anamuyang’ana ndipo anam’konda. Kenako anamuuza kuti: “Chinthu chimodzi chikusowekabe mwa iwe: Pita kagulitse zilizonse zimene uli nazo ndipo ndalama zake upatse osauka. Ukatero udzakhala ndi chuma kumwamba, ndiyeno ubwere udzakhale wotsatira wanga.”+
33 Gulitsani+ zinthu zanu ndi kupereka mphatso zachifundo.+ Dzipangireni zikwama za ndalama zomwe sizingathe, kutanthauza chuma chosatha kumwamba,+ kumene mbala singafikeko, ndipo njenjete* singawononge.
19 ndiponso asunge+ maziko abwino+ a tsogolo lawo monga chuma, kuti agwire mwamphamvu moyo weniweniwo.+