Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • Yesaya 6:10
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 10 Ukachititse anthu awa kuumitsa mtima wawo,+ ndipo ukachititse makutu awo kuti asamamve.+ Ukamate maso awo kuti asamaone ndi maso awowo, ndiponso kuti asamamve ndi makutu awo, komanso kuti mtima wawo usamvetsetse zinthu, kuti angatembenuke n’kuchira.”+

  • Mateyu 13:14
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 14 Ulosi wa Yesaya ukukwaniritsidwa pa iwowa, umene umati, ‘Kumva, mudzamva ndithu, koma osazindikira tanthauzo lake. Kuona, mudzaona ndithu, koma osazindikira.+

  • Maliko 4:12
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 12 kuti kupenya azipenya ndithu, koma osaona, ndi kuti kumva azimva ndithu, koma osazindikira tanthauzo lake, kutinso asatembenuke ndi kukhululukidwa.”+

  • Machitidwe 28:26
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 26 Mzimuwo unati, ‘Pita ukauze anthu awa kuti: “Kumva mudzamva ndithu, koma osazindikira ngakhale pang’ono. Kupenya mudzapenya ndithu, koma osaona ngakhale pang’ono.+

  • Aroma 11:8
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 8 monga mmene Malemba amanenera kuti: “Mulungu wawapatsa mzimu wa tulo tatikulu,+ maso osaona ndi makutu osatha kumva, kufikira lero.”+

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena