Salimo 50:15 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 15 Pa tsiku la nsautso undiitane.+Ine ndidzakulanditsa, ndipo iwe udzandilemekeza.”+ Yeremiya 33:3 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 3 ‘Mundiitane ndipo ndidzakuyankhani.+ Nthawi yomweyo ndidzakuuzani zinthu zazikulu ndi zovuta kuzimvetsa zimene simukuzidziwa.’”+ Maliko 11:24 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 24 N’chifukwa chake ndikukuuzani kuti, Pa zinthu zonse zimene mukupempherera ndi kupempha, khalani ndi chikhulupiriro ngati kuti mwazilandira kale, ndipo mudzazilandiradi.+ Yohane 15:7 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 7 Ngati mukhala ogwirizana ndi ine ndipo mawu anga akakhala mwa inu, mukhoza kupempha chilichonse chimene mukufuna ndipo chidzachitika kwa inu.+ Yakobo 1:6 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 6 Koma azipempha+ ndi chikhulupiriro, osakayikira m’pang’ono pomwe,+ pakuti wokayikira ali ngati funde lapanyanja lotengeka ndi mphepo+ ndi lowindukawinduka. 1 Yohane 3:22 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 22 ndipo chilichonse chimene tingapemphe, iye adzatipatsa,+ chifukwa tikusunga malamulo ake ndi kuchita zinthu zomukondweretsa.+ 1 Yohane 5:14 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 14 Ifetu timamudalira+ kuti chilichonse chimene tingamupemphe mogwirizana ndi chifuniro chake, amatimvera.+
3 ‘Mundiitane ndipo ndidzakuyankhani.+ Nthawi yomweyo ndidzakuuzani zinthu zazikulu ndi zovuta kuzimvetsa zimene simukuzidziwa.’”+
24 N’chifukwa chake ndikukuuzani kuti, Pa zinthu zonse zimene mukupempherera ndi kupempha, khalani ndi chikhulupiriro ngati kuti mwazilandira kale, ndipo mudzazilandiradi.+
7 Ngati mukhala ogwirizana ndi ine ndipo mawu anga akakhala mwa inu, mukhoza kupempha chilichonse chimene mukufuna ndipo chidzachitika kwa inu.+
6 Koma azipempha+ ndi chikhulupiriro, osakayikira m’pang’ono pomwe,+ pakuti wokayikira ali ngati funde lapanyanja lotengeka ndi mphepo+ ndi lowindukawinduka.
22 ndipo chilichonse chimene tingapemphe, iye adzatipatsa,+ chifukwa tikusunga malamulo ake ndi kuchita zinthu zomukondweretsa.+
14 Ifetu timamudalira+ kuti chilichonse chimene tingamupemphe mogwirizana ndi chifuniro chake, amatimvera.+