45 Kenako mwamsanga, Yesu analimbikitsa ophunzira ake kuti akwere ngalawa ndi kutsogola kupita kutsidya lina loyang’anizana nalo cha ku Betsaida. Koma iye anatsalira akuuza anthuwo kuti azipita kwawo.+
36 Yesu anayankha kuti:+ “Ufumu wanga suli mbali ya dziko lino.+ Ufumu wanga ukanakhala mbali ya dziko lino, atumiki anga akanamenya nkhondo+ kuti ndisaperekedwe kwa Ayuda. Koma ufumu wanga si wochokera pansi pano ayi.”
27 Kupembedza koyera+ ndi kosaipitsidwa+ kwa Mulungu ndi Atate wathu ndi uku: Kusamalira ana amasiye+ ndi akazi amasiye+ m’masautso awo,+ ndi kukhala wopanda banga+ la dzikoli.+