Mateyu 7:22 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 22 Ambiri adzati kwa ine pa tsiku limenelo, ‘Ambuye, Ambuye,+ kodi ife sitinalosere m’dzina lanu, ndi kutulutsa ziwanda m’dzina lanu, ndiponso kuchita ntchito zambiri zamphamvu m’dzina lanunso?’+ Machitidwe 21:20 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 20 Iwo atamva zimenezi anayamba kutamanda Mulungu, ndipo anamuuza kuti: “M’bale, kodi ukuona kuchuluka kwa okhulupirira amene ali pakati pa Ayuda? Ndipo onsewa ndi odzipereka pa nkhani yotsatira Chilamulo.+ Agalatiya 1:14 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 14 Ndinali kupita patsogolo kwambiri m’Chiyuda kuposa anzanga ambiri a fuko langa, omwe anali amsinkhu wanga.+ Pakuti ndinali wodzipereka kwambiri+ pa miyambo+ ya makolo anga. Afilipi 3:6 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 6 Kunena za kudzipereka, ndinali kuzunza mpingo.+ Kunena za chilungamo mwa kutsatira chilamulo, ndinakhaladi wopanda chifukwa chondinenezera.
22 Ambiri adzati kwa ine pa tsiku limenelo, ‘Ambuye, Ambuye,+ kodi ife sitinalosere m’dzina lanu, ndi kutulutsa ziwanda m’dzina lanu, ndiponso kuchita ntchito zambiri zamphamvu m’dzina lanunso?’+
20 Iwo atamva zimenezi anayamba kutamanda Mulungu, ndipo anamuuza kuti: “M’bale, kodi ukuona kuchuluka kwa okhulupirira amene ali pakati pa Ayuda? Ndipo onsewa ndi odzipereka pa nkhani yotsatira Chilamulo.+
14 Ndinali kupita patsogolo kwambiri m’Chiyuda kuposa anzanga ambiri a fuko langa, omwe anali amsinkhu wanga.+ Pakuti ndinali wodzipereka kwambiri+ pa miyambo+ ya makolo anga.
6 Kunena za kudzipereka, ndinali kuzunza mpingo.+ Kunena za chilungamo mwa kutsatira chilamulo, ndinakhaladi wopanda chifukwa chondinenezera.