Esitere
3 Pambuyo pake, Mfumu Ahasiwero analemekeza Hamani+ mwana wa Hamedata Mwagagi,+ ndipo anam’kweza+ ndi kum’patsa mpando wapamwamba kuposa akalonga ena onse amene mfumuyo inali nawo.+ 2 Choncho atumiki onse a mfumu amene anali kuchipata cha mfumu+ anali kuwerama ndi kugwadira Hamani, pakuti mfumu inali italamula kuti anthu azim’chitira zimenezi. Koma Moredekai sanali kumuweramira kapena kumugwadira.+ 3 Ndiyeno atumiki a mfumu amene anali kuchipatako anayamba kufunsa Moredekai kuti: “N’chifukwa chiyani ukunyalanyaza lamulo la mfumu?”+ 4 Popeza kuti anali kulankhula naye tsiku ndi tsiku koma sanali kuwamvera, anthuwo anakauza Hamani kuti aone ngati Moredekai angapitirize zimene anali kuchitazo,+ pakuti anawauza kuti anali Myuda.+
5 Hamani anakwiya kwambiri+ chifukwa anaona kuti Moredekai sanali kumuweramira ndi kumugwadira.+ 6 Koma Hamani anaona kuti n’zosakwanira kupha Moredekai yekha pakuti anthu anamuuza za anthu a mtundu wa Moredekai. Choncho Hamani anayamba kufunafuna kufafaniza+ Ayuda onse, anthu a mtundu wa Moredekai amene anali mu ufumu wonse wa Ahasiwero.+
7 Ndiyeno m’mwezi woyamba,+ umene ndi mwezi wa Nisani,* m’chaka cha 12+ cha Mfumu Ahasiwero, munthu wina anachita Puri*+ kapena kuti Maere+ pamaso pa Hamani kuti adziwe tsiku ndi mwezi woyenerera. Choncho Maerewo anagwera mwezi wa 12 umene ndi mwezi wa Adara.*+ 8 Kenako Hamani anauza Mfumu Ahasiwero kuti: “Pali mtundu wina wa anthu umene ukupezeka paliponse+ ndipo ukudzipatula pakati pa anthu m’zigawo zonse za ufumu wanu.+ Malamulo awo ndi osiyana ndi malamulo a anthu ena onse ndipo sakutsatira+ malamulo anu mfumu. Choncho si bwino kuti inu mfumu muwalekerere anthu amenewa. 9 Ngati zingakukomereni mfumu, palembedwe makalata kuti anthu amenewa awonongedwe. Ine ndidzapereka matalente 10,000+ asiliva kwa anthu amene adzagwira ntchito imeneyi+ kuti abweretse matalentewo mosungiramo chuma cha mfumu.”
10 Pamenepo mfumu inavula mphete yodindira+ kudzanja lake ndi kuipereka kwa Hamani+ mwana wa Hamedata Mwagagi,+ amene anali kudana kwambiri ndi Ayuda.+ 11 Ndiyeno mfumu inauza Hamani kuti: “Siliva+ akhale wako, pamodzinso ndi anthuwa ndipo uchite nawo zimene ukuona kuti n’zabwino.”+ 12 Kenako anaitana alembi a mfumu+ m’mwezi woyamba, pa tsiku la 13 la mweziwo. Ndipo alembiwo analemba+ zonse zimene Hamani analamula masatarapi* a mfumu, abwanamkubwa a m’zigawo zosiyanasiyana+ za ufumuwo ndi akalonga a anthu osiyanasiyana m’chigawo chilichonse. Makalata amenewa anawalemba malinga ndi mmene anthu a m’chigawo chilichonse anali kulembera+ ndiponso m’chinenero chawo. Makalatawa anawalemba m’dzina+ la Mfumu Ahasiwero ndipo anawadinda ndi mphete yake yodindira.+
13 Ndiyeno anatumiza makalatawo kudzera mwa amtokoma+ kupita kuzigawo zonse za mfumu. Anachita izi kuti pa tsiku limodzi,+ pa tsiku la 13 la mwezi wa 12 umene ndi mwezi wa Adara,+ awononge, aphe ndi kufafaniza Ayuda onse, mnyamata komanso mwamuna wachikulire, ana ndi akazi ndi kufunkha zinthu zawo.+ 14 Zimene analemba m’makalatawo kuti zikhale lamulo+ kuzigawo zonse,+ anazifalitsa kwa anthu a mitundu yonse kuti akonzekere tsiku limeneli. 15 Amtokomawo anapita mofulumira+ chifukwa cha mawu a mfumu ndi lamulo limene linaperekedwa m’nyumba ya mfumu yokhala ndi mpanda wolimba kwambiri ya ku Susani.+ Ndipo mfumu ndi Hamani, anakhala pansi kuti amwe vinyo,+ koma mumzinda wa Susani+ munali chipwirikiti.+