-
Ekisodo 29:10-14Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
10 Kenako ubweretse ngʼombe patsogolo pa chihema chokumanako, ndipo Aroni ndi ana ake aike manja awo pamutu wa ngʼombeyo.+ 11 Ndiyeno ngʼombeyo uiphe pamaso pa Yehova, pakhomo la chihema chokumanako.+ 12 Ukatero utengeko magazi a ngʼombeyo ndi chala chako ndipo uwapake panyanga za guwa lansembe.+ Magazi otsalawo uwathire pansi pa guwa lansembe.+ 13 Kenako utenge mafuta onse+ okuta matumbo, mafuta apachiwindi, impso ziwiri ndi mafuta ake nʼkuzitentha kuti paguwa lansembe pakhale utsi.+ 14 Koma nyama ya ngʼombeyo, chikopa chake ndi ndowe zake uzitenthe ndi moto kunja kwa msasa. Ngʼombeyo ndi nsembe yamachimo.
-
-
Levitiko 4:3, 4Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
3 Ngati wansembe wodzozedwa+ wachita tchimo+ ndipo lapangitsa anthu onse kupalamula, azipereka kwa Yehova ngʼombe yaingʼono yamphongo yopanda chilema monga nsembe yamachimo chifukwa cha tchimo lakelo.+ 4 Azibweretsa ngʼombe yamphongoyo pamaso pa Yehova pakhomo la chihema chokumanako+ ndipo aziika dzanja lake pamutu wa ngʼombeyo, kenako aziipha pamaso pa Yehova.+
-