Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • km 3/97 tsamba 2
  • Misonkhano Yautumiki ya March

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Misonkhano Yautumiki ya March
  • Utumiki Wathu wa Ufumu—1997
  • Timitu
  • Mlungu Woyambira March 3
  • Mlungu Woyambira March 10
  • Mlungu Woyambira March 17
  • Mlungu Woyambira March 24
  • Mlungu Woyambira March 31
Utumiki Wathu wa Ufumu—1997
km 3/97 tsamba 2

Misonkhano Yautumiki ya March

Mlungu Woyambira March 3

Nyimbo Na. 53

Mph. 10: Zilengezo zapamalopo. Zilengezo zosankhidwa mu Utumiki Wathu Waufumu. Limbikitsani onse kuyamba kuitanira okondwerera ku Chikumbutso pa March 23. Sonyezani kope la chiitano cha ku Chikumbutso, ndipo limbikitsani onse kukhala ndi mtokoma wawo ndi kuyamba kugaŵira ziitanozo mlungu uno.

Mph. 15: “Mangirirani Nyumba Yanu.” Mafunso ndi mayankho. Phatikizanipo zokumana nazo za mu 1995 Yearbook, tsamba 228.

Mph. 20: “Kuthandiza Mabanja Kumanga Mtsogolo Mokhalitsa.” (Ndime 1-5) Lankhulanipo mwachidule pandime 1, ndiyeno lankhulani mmene chidwi chingakulitsidwire pa buku la Chimwemwe cha Banja mwa kugwiritsira ntchito mitu yake, zithunzi zokongola, ndi mabokosi a mafunso openda. Ofalitsa okhoza achitire chitsanzo maulaliki a m’ndime 2-5. Limbikitsani onse kuyesetsa ndithu kugaŵira bukuli mabanja amene nthaŵi yapita anasonyeza chidwi. Kumbukirani kutchula chopereka chamasiku onse.

Nyimbo Na. 71 ndi pemphero lomaliza.

Mlungu Woyambira March 10

Nyimbo Na. 56

Mph. 10: Zilengezo zapamalopo. Lipoti la maakaunti. Kumbutsani onse kutsimikiza kuti adzatsatira kuŵerenga Baibulo kwa Chikumbutso kwa pa March 18-23, kosonyezedwa m’kabuku ka Kusanthula Malemba Tsiku ndi Tsiku.

Mph. 20: “Khalani Akuyamika.” Mafunso ndi mayankho. Onse ayenera kuyesetsa moona mtima kuitanira ku Chikumbutso maphunziro a Baibulo, okondwerera, achibale okondedwa, ndi abale ndi alongo alionse amene sakugwirizana ndi mpingo mwachangu. Chitsanzo cha wofalitsa akuitanira wokondedwa ku Chikumbutso. Wonjezeranipo ndemanga za mu Nsanja ya Olonda ya July 1, 1988, tsamba 11, ndime 16-17. Limbikitsani onse amene angathe kuchita upainiya wothandiza kuti achite motero m’April ndi May.

Mph. 15: “Kuthandiza Mabanja Kumanga Mtsogolo Mokhalitsa.” (Ndime 6-8) Perekani malingaliro ena osonyeza mmene tingagaŵire buku la Chimwemwe cha Banja pochita ulaliki wamwamwaŵi pantchito, kusukulu, m’paki, kapena m’zoyendera za onse, limodzinso ndi pochezera achibale. Wofalitsa wokhoza achitire chitsanzo maulaliki a m’ndime 6 ndi 7. Kukambitsirana paulendo wobwereza kuyenera kumthandiza munthu kuzindikira mmene phunziro la Baibulo lingalimbitsire maunansi a m’banja. Maphunziro ayenera kuchititsidwa m’brosha lakuti Kodi Mulungu Amafunanji kwa Ife?, ndi cholinga cha kusamukira ku buku la Chidziŵitso, kapena phunzirolo lingayambike m’buku la Chidziŵitso lenilenilo.

Nyimbo Na. 72 ndi pemphero lomaliza.

Mlungu Woyambira March 17

Nyimbo Na. 63

Mph. 15: Zilengezo zapamalopo. Pendani “Zikumbutso za pa Chikumbutso,” ndi kutchula makonzedwe apamalopo a Chikumbutso. Onse ayenera kupanga makonzedwe omaliza a kuthandiza ophunzira Baibulo ndi okondwerera kudzapezekapo.

Mph. 15: Zosoŵa zapamalopo. Kapena nkhani ya mkulu pankhani yakuti “Kodi Mufunikiradi Kupepesa?” ya mu Nsanja ya Olonda ya September 15, 1996, masamba 22-4.

Mph. 15: Igwiritsireni Ntchito Bwino 1997 Yearbook of Jehovah’s Witnesses. Tate apenda nkhani zopezeka pamasamba 3-9 ndi banja lake. Asonyeza chifukwa chake timakondwera kuona kupita patsogolo kwa teokrase kuzungulira dziko lonse lapansi. Tate alongosola mmene m’chaka chikudzacho, angapatulire mphindi zingapo tsiku lililonse panthaŵi yachakudya kuti aziŵerenga Yearbook mopita patsogolo limodzinso ndi kukambitsirana lemba latsiku.

Nyimbo Na. 75 ndi pemphero lomaliza.

Mlungu Woyambira March 24

Nyimbo Na. 67

Mph. 9: Zilengezo zapamalopo. Fotokozani kuti nthaŵi yofunsira upainiya wothandiza m’April idakalipo. Longosolani mwachidule makonzedwe apamalopo owonjezera amene akupangidwa kaamba ka kukumana kwa utumiki m’mweziwu.

Mph. 24: “Msonkhano Wachigawo wa 1997 wa ‘Kukhulupirira Mawu a Mulungu’ wa Mboni za Yehova.” Mafunso ndi mayankho. (Ndime 1-9) Ŵerengani ndime zonse ndi malemba onse. Yokambidwa ndi mlembi. Monga mwaonera m’nkhaniyo, gogomezerani mapulinsipulo a Baibulo otsatirira zitsogozo za Sosaite pankhani ya zipinda. Yamikirani abale kaamba ka kutsatira makonzedwe a Sosaite a zipinda.

Mph. 12: Kuthandiza Wofalitsa Watsopano Kuyamba. Pendani ndime 19 m’mphatika ya Utumiki Wathu Waufumu wa June 1996. Chitani chitsanzo cha mmene wofalitsa wokhoza amakonzekeretsera wophunzira Baibulo amene wangoikidwa kumene ndi akulu kukhala wofalitsa wosabatizidwa. Apendera limodzi buku la Uminisitala Wathu, tsamba 111, ndime 2. Wofalitsa wachidziŵitsoyo atchula zimene angakumane nazo pokhala ndi phande mu umboni wakunyumba ndi nyumba ndi kutinso sayenera kulefuka ngati ambiri salabadira. Wofalitsa asimba chokumana nacho chosonyeza chisangalalo chimene chimakhalapo titapeza munthu woona mtima amene amvetsera. Akonzera limodzi ulaliki wa magazini wachidule ndipo wosavuta kenako auyeseza. Amyamikira molimbikitsa ndipo apanga makonzedwe otsimikizika a kukhala ndi phande limodzi mu utumiki mlungu uno.

Nyimbo Na. 89 ndi pemphero lomaliza.

Mlungu Woyambira March 31

Nyimbo Na. 70

Mph. 15: Zilengezo zapamalopo. Kumbutsani onse kupereka malipoti awo a utumiki wakumunda wa March. Lengezani maina a onse amene adzachita upainiya wothandiza m’April. Pendani Bokosi la Mafunso. Pokambitsirana Bokosi la Mafunso limeneli, ŵerengani ndi kukambitsirana chilengezo chomaliza chonena za maliro.

Mph. 20: “Msonkhano Wachigawo wa 1997 wa ‘Kukhulupirira Mawu a Mulungu’ wa Mboni za Yehova.” Mafunso ndi mayankho. (Ndime 10-18) Limbikitsani onse kukhala ndi khalidwe loyenerera nyumba ya Mulungu pamene afika pamsokhano. Ŵerengani ndime zonse ndi malemba ake. Yokambidwa ndi mkulu woyenerera.

Mph. 10: Pendani Zogaŵira za m’April. Gaŵirani makope a Nsanja ya Olonda ndi Galamukani! Longosolani mwachidule malingaliro a m’ndime 3, 4, ndi 8 patsamba 8 la Utumiki Wathu Waufumu wa October 1996 mmene tingakonzere ulaliki wa magazini. Ofalitsa aŵiri achitire chitsanzo ulaliki umodzi kapena maulaliki aŵiri achidule ndi kutchula chopereka chanthaŵi zonse. Ofalitsa ayenera kulemba awo amene amalandira magazini ndi kuwawonjezera panjira yawo ya magazini.

Nyimbo Na. 92 ndi pemphero lomaliza.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena