Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • km 7/06 tsamba 2
  • Ndandanda ya Misonkhano ya Utumiki

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Ndandanda ya Misonkhano ya Utumiki
  • Utumiki Wathu wa Ufumu—2006
  • Timitu
  • Mlungu Woyambira July 10
  • Mlungu Woyambira July 17
  • Mlungu Woyambira July 24
  • Mlungu Woyambira July 31
  • Mlungu Woyambira August 7
Utumiki Wathu wa Ufumu—2006
km 7/06 tsamba 2

Ndandanda ya Misonkhano ya Utumiki

Dziwani Izi: M’miyezi ikubwerayi Utumiki Wathu wa Ufumu uzikhalabe ndi ndandanda ya Misonkhano ya Utumiki ya mlungu uliwonse. Mipingo ingasinthe ndandanda moyenera kuti ikapezeke pa Msonkhano Wachigawo wakuti “Chipulumutso Chayandikira.” Ngati n’koyenera, gwiritsani ntchito mphindi 15 pa Msonkhano wa Utumiki womaliza musanapite ku msonkhano wachigawo kuti muonenso malangizo oyenera ndi zikumbutso za mu mphatika ya Utumiki Wathu wa Ufumu uno zimene zikukhudza mpingo wanuwo. Pakadutsa mwezi umodzi kapena iwiri utatha msonkhano wachigawo, gwiritsani ntchito mphindi 15 mpaka 20 za mu Msonkhano wa Utumiki (mwina mungagwiritse ntchito chigawo cha zosowa za pampingo) kuti mubwereze mfundo zazikulu za msonkhano wachigawo. Cholinga chake si kubwereza zinthu zonse zimene zinakambidwa pa msonkhano ayi. M’malo mwake kambiranani mbali zokhazo zomwe zikukhudza ntchito ya utumiki wa kumunda. Pemphani omvera kufotokoza mmene akugwiritsira ntchito mfundozo mu utumiki wawo.

Mlungu Woyambira July 10

Nyimbo Na. 4

Mph. 8: Zilengezo za pampingo. Pogwiritsa ntchito ulaliki umene uli patsamba 8 kapena ulaliki wina uliwonse umene ungakhale wothandiza m’gawo lanu, chitani zitsanzo zosonyeza zimene tinganene pogawira Nsanja ya Olonda ya July 15 ndi Galamukani! ya July. M’chitsanzo chimodzi, sonyezani mmene tingayankhire anthu amene akufuna kuti tisakambirane nawo mwa kunena kuti: “Ndife Akristu kale pano.” (Onani m’buku la Kukambitsirana, tsa. 19.) (Ngati mpingo wanu sunalandire magazini tatchulawa gwiritsirani ntchito zitsanzo zimene zinatchulidwa mu Utumiki Wathu wa Ufumu wa mwezi watha.)

Mph. 20: “Dikirani Yehova.”a Ikambidwe ndi mlembi wa mpingo. Tchulani msonkhano wachigawo womwe mpingo wanu udzapite. Pemphani omvera kuti afotokoze mmene kuvala baji yathu ya msonkhano nthawi zonse pamene tili m’dera lochitikira msonkhanowo kungatsegulire mwayi wolalikira. Limbikitsani omvera kuti azikalalikira mwamwayi paliponse pamene papezeka mpata ndiponso kuti akagwiritse ntchito fomu ya Kaonaneni ndi Wachidwi Uyu (S-43) podziwitsa ena za munthu wachidwi aliyense amene akumana naye. Kambiranani za m’bokosi lakuti “Zofunika Kukumbukira pa Msonkhano Wachigawo.”

Mph. 17: “Thandizani Ophunzira Baibulo Kuyamikira Makhalidwe Osayerekezereka a Yehova.”b Phatikizanipo chitsanzo chosonyeza mmene tingagwiritsire ntchito mafunso pothandiza wophunzira Baibulo kuganizira mfundo za m’bokosi la kubwereza la kumapeto kwa mutu woyamba m’buku la Baibulo Limaphunzitsa Chiyani.

Nyimbo Na. 88 ndi pemphero lomaliza.

Mlungu Woyambira July 17

Nyimbo Na. 99

Mph. 10: Zilengezo za pampingo. Zilengezo zina musankhe mu Utumiki Wathu wa Ufumu uno. Fotokozani mwachidule mawu a patsamba 32, la Nsanja ya Olonda ya August 15, 2000. Sonyezani phindu lowerenga Baibulo tsiku ndi tsiku, ngakhale pamene tili pa tchuthi kapena pamene tikuchita zinthu zina zosiyana ndi zimene timachita nthawi zonse.

Mph. 25: “Kuimba Zitamando Ndi Mbali Yofunika ya Kulambira Kwathu.”c

Mph. 10: “Kugulitsa Malonda pa Misonkhano Yathu Yachigawo.” Nkhani ndi kukambirana ndi omvera. Tsindikani mfundo ya kufunika kobweretsa nkhomaliro yopepuka m’malo mochoka pamalo a msonkhano wachigawo kupita kukagula chakudya kwa ogulitsa chakudya m’misewu ndi ku malesitilanti a pafupi ndi malo a msonkhanowo.

Nyimbo Na. 189 ndi pemphero lomaliza.

Mlungu Woyambira July 24

Nyimbo Na. 218

Mph. 15: Zilengezo za pampingo. Werengani lipoti la maakaunti ndi mawu oyamikira zopereka amene alembedwa pa sitetimenti. Pogwiritsa ntchito ulaliki womwe uli patsamba 8 kapena ulaliki wina uliwonse umene ungakhale wothandiza m’gawo lanu, chitani zitsanzo zosonyeza zimene tinganene pogawira Nsanja ya Olonda ya August 1 ndi Galamukani! ya August. Pamapeto pa chitsanzo chilichonse, bwerezani mawu oyamba amene agwiritsidwa ntchito podzutsa chidwi cha mwini nyumba. (Ngati mpingo wanu sunalandire magazini tatchulawa gwiritsirani ntchito zitsanzo zimene zinatchulidwa mu Utumiki Wathu wa Ufumu wa mwezi watha.)

Mph. 10: “Anasonyeza Chitsanzo cha Kukhulupirika.” Nkhani yokhala ndi zokumana nazo zingapo zimene zalembedwapo m’mabuku athu za apainiya apadera kapena mafunso ofunsa apainiya apadera amene akutumikira mu mpingo wanu.—Onani Watch Tower Publications Index pa mutu wakuti, “Special Pioneers.”

Mph. 20: “Tsanzirani Mulungu Wathu Wachisangalalo, Yehova.”d Pemphani omvera kuti afotokoze zimene zawathandiza kuti apitirizebe kukhala osangalala ndi amtima wabwino polalikira m’gawo lawo.

Nyimbo Na. 12 ndi pemphero lomaliza.

Mlungu Woyambira July 31

Nyimbo Na. 28

Mph. 10: Zilengezo za pampingo. Kumbutsani ofalitsa kupereka malipoti a utumiki wa kumunda a mwezi wa July. Tchulani mabuku ogawira mu August.

Mph. 15: Kakonzedwe ndi Kayendetsedwe ka Mpingo. Nkhani ndi kukambirana ndi omvera kuchokera m’buku la Gulu Lochita Chifuniro cha Yehova, mutu 4.

Mph. 20: “Kulitsani Zizolowezi Zabwino Ndipo Mudzapindula Kwambiri.”e Pemphani omvera kuti afotokoze mmene ayesetsera kupanga ndi kutsatira ndandanda yabwino yochitira zinthu zauzimu ndi madalitso amene apeza chifukwa chochita zimenezi.

Nyimbo Na. 130 ndi pemphero lomaliza.

Mlungu Woyambira August 7

Nyimbo Na. 209

Mph. 10: Zilengezo za pampingo. Fotokozani mwachidule mmene zitsanzo za maulaliki a mu Utumiki Wathu wa Ufumu zingasinthidwire kuti zigwirizane ndi zosowa za m’gawo lanu.—Onani Utumiki Wathu wa Ufumu wa January 2005, tsa. 8.

Mph. 15: Misonkhano Imene Imafulumiza ku Chikondano ndi Ntchito Zabwino. Nkhani yotengedwa mu Nsanja ya Olonda ya March 15, 2002, tsamba 24 ndi 25. Mwachidule, funsani wofalitsa kuti afotokoze khama limene wachita kuti azipezeka pa misonkhano nthawi zonse ndi mmene wapindulira pochita zimenezo.

Mph. 20: Khalani Opita Patsogolo ndi Otha Kusintha mu Utumiki. Nkhani ndi kukambirana ndi omvera yotengedwa mu Nsanja ya Olonda ya December 1, 2005, tsamba 28 mpaka 30. M’nkhani yochoka pa ndime 6 mpaka 11, sonyezani mmene Paulo analili watcheru, wotha kusintha, ndi waluso pamene ankalalikira ndi kuphunzitsa. Ndiyeno pemphani omvera kuti ayankhe mafunso kuyambira ndime 12 mpaka 14, powagwirizanitsa ndi gawo lanu. Phatikizanipo chitsanzo chosonyeza mmene ofalitsa angasinthire ulaliki wawo mu utumiki, poganizira zosowa, moyo ndi chikhalidwe cha anthu a m’gawo lanu.

Nyimbo Na. 83 ndi pemphero lomaliza.

[Mawu a M’munsi]

a Kambani mawu oyamba osakwana mphindi imodzi, ndiyeno kambiranani mwa mafunso ndi mayankho.

b Kambani mawu oyamba osakwana mphindi imodzi, ndiyeno kambiranani mwa mafunso ndi mayankho.

c Kambani mawu oyamba osakwana mphindi imodzi, ndiyeno kambiranani mwa mafunso ndi mayankho.

d Kambani mawu oyamba osakwana mphindi imodzi, ndiyeno kambiranani mwa mafunso ndi mayankho.

e Kambani mawu oyamba osakwana mphindi imodzi, ndiyeno kambiranani mwa mafunso ndi mayankho.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena