Uthenga Wa Ufumu wa Panthaŵi Yake Woyenera Kufalitsidwa pa Dziko Lonse
1 Pa Sande, April 23, nkhani yapoyera yapadera idzaperekedwa ya mutu wochititsa chidwi wakuti “Mapeto a Chipembedzo Chonyenga Ali Pafupi.” Kumapeto kwa msonkhano umenewu patsikulo, Uthenga wa Ufumu wa masamba anayi wosonkhezera maganizo udzatulutsidwa. Uthenga wa panthaŵi yake umenewu udzafalitsidwa padziko lonse mkati mwa nyengo ya milungu itatu kuyambira pa April 24 mpaka May 14.
2 M’mbali zonse za dziko lapansi, anthu ali othedwa nzeru. Mosasamala kanthu za kumene amakhala, iwo akuyang’anizana ndi mavuto ochuluka. Uthenga wa Ufumu udzakhala wokondweretsa kwambiri kwa awo amene alidi odera nkhaŵa ndi zimene zikuchitika, popeza kuti udzawatsogoza ku Mawu a Mulungu monga magwero odalirika a chitsogozo cha munthu. (Sal. 119:105) Tonsefe tikuyembekezera ndi chidwi kudzakhala ndi kope la Uthenga wa Ufumu pamene utulutsidwa pa April 23. Pakali pano, padakali zambiri zimene ziyenera kuchitidwa kukonzekera mkupiti waukulu umenewu wa milungu itatu.
3 Limbikitsani Onse Kukhala ndi Phande Mwachangu: Kodi ndani amene ayenera kukhala ndi phande m’ntchito imeneyi? Ndithudi aliyense amene ali kale wofalitsa adzakhala wofunitsitsa kutero! Bwanji ponena za ophunzira Baibulo amene amafika pamisonkhano ya mpingo mokhazikika? Ena ayanjana nafe kwa nthaŵi yotalikirapo ndipo akupanga kupitabe patsogolo mosalekeza. Ngati iwo agwirizanitsa miyoyo yawo ndi ziphunzitso za Malemba, kodi ali oyenera kuŵerengeredwa monga olengeza Ufumu? Wofalitsa amene akuchititsa phunziro la Baibulo angakambitsirane nkhaniyo ndi wophunzirayo, ndipo ngati wophunzirayo akukhumba kukhala ndi phande mu utumiki wakumunda, akulu aŵiri adzapenda naye mfundo zimene zili pamasamba 98 ndi 99 a buku la Olinganizidwa Kutsiriza Uminisitala Wathu. Chimenechi chiyenera kuchitidwa mwamsanga kotero kuti awo amene ali oyenera kukhala ofalitsa osabatizidwa adzakhale ndi phande lokwanira mu mkupiti umenewu. Ophunzira Baibulo amene sali kale oyenera kukhala ofalitsa osabatizidwa angalimbikitsidwebe kugaŵira Uthenga wa Ufumu umenewu kwa mabwenzi awo kapena ziŵalo za banja.—Onani Nsanja ya Olonda, November 15, 1988, tsamba 17, ndime 8.
4 Ntchito imeneyi njosavuta; aliyense angakhalemo ndi phande. Makolo angaphatikizepo magawo a kuyeseza ndi Uthenga wa Ufumu monga mbali ya phunziro lawo la banja la Baibulo la mlungu ndi mlungu kotero kuti ziŵalo zonse za banja zikhale zokonzekera bwino kuugaŵira kunyumba ndi nyumba. Nthaŵi zonse ulaliki wosavuta umakhala wabwino koposa. Mutakamba mawu oyamba achidule, gaŵirani Uthenga wa Ufumu kwa mwininyumba, ndi kumlimbikitsa kuuŵerenga. Pamene eninyumba asonyeza chikondwerero, lembani zimenezo kuti mudzabwerenso kudzakulitsa chikondwererocho. (1 Akor. 3:6, 7) Mfungulo ya chipambano ndiyo ulaliki wosavuta, wokonzekeredwa bwino.
5 Padzakhala “zochita zochuluka” mu April ndi May. M’kope la Utumiki Wathu Waufumu wa mwezi wamaŵa, chidziŵitso chowonjezereka chidzaperekedwa m’mphatika ya mutu wakuti “Zochita Zochuluka m’Ntchito ya Ambuye.”—1 Akor. 15:58, NW.