M’mwezi wa November Tidzagwira Ntchito Yogawira Kapepala ka Uthenga wa Ufumu Na. 38
1. Pa nkhani ya akufa, kodi anthu amakhala ndi mafunso otani, ndipo n’chiyani chidzathandize kuyankha mafunsowa m’mwezi wa November?
1 Ngakhale kuti anthu amakhulupirira zinthu zosiyanasiyana, imfa ndi mdani wa anthu onse. (1 Akor. 15:26) Munthu akamwalira, anthu ambiri amadzifunsa kuti, ‘Kodi wapita kuti? Kodi tidzamuonanso?’ Choncho kwa mwezi wathunthu, mipingo yonse ya Mboni za Yehova padziko lonse idzagwira ntchito yogawira kapepala ka Uthenga wa Ufumu Na. 38, kamutu wakuti “Kodi N’zoona Kuti Akufa Adzauka?” Tidzayamba kugwira ntchito yapaderayi pa November 1, ndipo ntchitoyi ikadzatha, tidzapitiriza kugawira kapepalaka mu utumiki ngati mmene timachitira ndi timapepala tina tonse.
2. Kodi kapepala ka Uthenga wa Ufumu Na. 38, kakonzedwa bwanji?
2 Kodi Kapepalaka Kakonzedwa Bwanji?: Kapepala ka Uthenga wa Ufumu Na. 38, kakonzedwa moti munthu azitha kukapinda m’njira yakuti patsamba loyamba pazioneka mutu womwe ndi wochititsa chidwi komanso mawu akuti, “Kodi mungayankhe kuti . . . inde? ayi? mwinamwake?” Munthu akatsegula kapepala ka Uthenga wa Ufumu kameneka, azitha kuona zimene Baibulo limanena poyankha funso lomwe ndi mutu wa kapepalaka. Azithanso kuona zimene iyeyo angachite kuti adzalandire madalitso amene Mulungu analonjeza m’Baibulo. Angaonenso zifukwa zomuchititsa kukhulupirira Baibulo. Patsamba lomaliza la kapepalaka pali funso lochititsa chidwi lomwe munthuyo angaliganizire komanso limene lingamulimbikitse kuti apitirize kuphunzira zambiri.
3. Kodi ntchito yapadera yogawira timapepala ta Uthenga wa Ufumu Na. 38, tidzaigwira bwanji?
3 Kodi Tidzakagawira Bwanji?: Tidzagwira ntchito yogawira kapepalaka ngati mmene timachitira pogawira timapepala toitanira anthu ku Chikumbutso kapena kumsonkhano wachigawo. Akulu adzafotokoza mmene tidzagwirire ntchitoyi m’gawo lonse la mpingo wathu, motsatira malangizo amene analandira m’kalata ya pa April 1, 2013. Mipingo imene ili ndi gawo laling’ono ingapemphe kuti ithandize mipingo yapafupi yomwe ili ndi gawo lalikulu. Mukamatenga timapepala ta Uthenga wa Ufumu Na. 38 pamalo otengera mabuku, muzikumbukira kutenga timapepala timene mungagawire kwa mlungu umodzi basi. Ngati mungamalize kugawira timapepalati kunyumba ndi nyumba m’gawo lanu lonse mwezi wa November usanathe, mungayambe kugawira timapepalati mukamalalikira kumalo omwe kumapezeka anthu ambiri. Komanso ngati timapepalati tingathe mwezi wa November usanathe, mungapitirize kugawira mabuku amene asonyezedwa kuti mugawire m’mweziwo. Pa Loweruka loyambirira la mweziwu, tidzagwira ntchito yogawira timapepalati m’malo moyambitsa maphunziro a Baibulo. Pa masiku ena onse a Loweruka ndi Lamlungu, tizidzagawiranso magazini tikaona kuti n’zofunikira kutero. Choncho, tikukulimbikitsani kuti mukonzeretu mapulani n’cholinga choti mudzagwire nawo ntchito yapadera yogawira timapepalati.