Zitsanzo za Ulaliki
Nsanja ya Olonda December 1
“Anthu ambiri amakhala ndi maganizo olakwika pa nkhani ya Baibulo. N’zoona kuti amalilemekeza koma amaona kuti ndi lovuta kulimvetsa. Inuyo mumaliona bwanji? [Yembekezerani ayankhe.] Tiyeni tiwerenge Aroma 15:4 kuti tione chifukwa chake tiyenera kumvetsa Baibulo. [Werengani.] Magaziniyi ikusonyeza kuti Baibulo linalembedwa m’njira yoti tizilimvetsa komanso ikufotokoza zimene tingachite kuti tizilimvetsa.”
Galamukani! December
“Tikukambirana ndi anthu nkhani yothandiza kwambiri mabanja. Aliyense amafuna kuti azikhala mwamtendere m’banja. Kodi n’zotheka kuti anthu m’banja asamasiyane maganizo? Ngati n’zosatheka, kodi tingatani kuti tizithetsa bwino kusiyana maganizo? [Yembekezerani ayankhe.] Tiyeni tione zimene Baibulo limanena pa Miyambo 26:20. [Werengani.] Magaziniyi ikufotokoza malangizo opezeka m’Baibulo amene angathandize mabanja kukhala mwamtendere.”