Kuwonjezera Luso Lathu mu Utumiki—Kuyambitsa Phunziro Lachidule Pogwiritsa Ntchito Kabuku ka Uthenga Wabwino Wochokera kwa Mulungu
N’chifukwa Chiyani Kuchita Zimenezi N’kofunika? Kuti tithandize anthu kukhala ophunzira a Yesu, tiyenera kuwaphunzitsa Mawu a Mulungu. (Mat. 28:19, 20) Tonsefe tikhoza kukwanitsa kuphunzitsa anthu Mawu a Mulungu ngati titagwiritsa ntchito mabuku omwe tili nawo. Kabuku ka Uthenga Wabwino Wochokera kwa Mulungu kanakonzedwa n’cholinga choti katithandize pophunzitsa ena. Ndipotu tikhoza kugwiritsa ntchito kabukuka kuti tiyambitse phunziro la Baibulo lachidule pamene takumana ndi munthu koyamba.
Tayesani Kuchita Izi Mwezi Uno:
Pemphani Yehova kuti akuthandizeni kupeza munthu woti muziphunzira naye Baibulo. Mungamupemphenso kuti akuthandizeni kuti muziphunzitsa mogwira mtima.—Afil. 2:13.
Mukamaphunzira Baibulo panokha kapena mukamachita kulambira kwa pabanja mungachite bwino kuyeserera chitsanzochi. Kuchita zimenezi kungakuthandizeni kuti muzilankhula molimba mtima komanso kuyambitsa phunziro la Baibulo lachidule mukakhala mu utumiki.