Muziponya Nkhonya Zanu Mwanzeru
1. Kodi lemba la 1 Akorinto 9:26 limagwirizana bwanji ndi utumiki wathu?
1 Mtumwi Paulo analemba kuti: “Sikuti ndikungothamanga osadziwa kumene ndikulowera. Mmene ndikuponyera nkhonya zanga, sikuti ndikungomenya mphepo ayi.” (1 Akor. 9:26) Pamenepa, Paulo ankafotokoza za kufunika koika maganizo ake onse pa kukwaniritsa zolinga zake zauzimu. Komabe, mawu amenewa tingawagwiritsenso ntchito ponena za utumiki wathu. Ifenso tikufuna kuponya “nkhonya” zathu kapena kuchita zinthu mwanzeru kuti tikwanitse kuchita zinthu zambiri. Koma tingachite bwanji zimenezi?
2. Kodi tingatsanzire bwanji Paulo ndi Akhristu ena oyambirira posankha nthawi ndiponso malo olalikira?
2 Muzipita Kumene Kuli Anthu: Paulo ndi Akhristu ena oyambirira ankalalikira kumene ankayembekezera kupeza anthu. (Mac. 5:42; 16:13; 17:17) Choncho ngati anthu ambiri m’gawo lathu amapezeka pakhomo chakumadzulo, imeneyi ingakhale nthawi yabwino kuchita ulaliki wa nyumba ndi nyumba. Kodi kumalo okwerera basi kapena sitima kumakhala anthu ambiri m’mawa kapena chakumadzulo pamene anthu akupita ku ntchito kapena kuweruka? Kodi ndi nthawi iti pamene kumalo amalonda a m’gawo lanu kumakhala anthu ambiri? Mungachite ulaliki wa mumsewu wogwira mtima nthawi zimenezi.
3. Fotokozani njira zimene tingaponyere nkhonya zathu mwanzeru pamene tikulalikira m’gawo lathu.
3 Muzilalikira M’gawo Lanu Mwanzeru: Tiyenera kuchita zinthu mosamala kuti tiziponya nkhonya zathu mwanzeru pamene tikulalikira m’gawo lathu. Mwachitsanzo, m’malo mokhala ndi gulu lalikulu polalikira m’dera limodzi, zimene zingafune khama komanso nthawi yambiri kuti muchite zinthu mwadongosolo, zingakhale bwino kugawa gululo. N’chimodzimodzinso pamene mukulalikira m’dera lakutali. Tikhoza kulalikira dera lalikulu mofulumira ndiponso kukhala ndi mipata yambiri yolankhula ndi anthu ngati tayenda m’magulu ang’onoang’ono. Zingakhalenso bwino ngati titapempha kukhala ndi gawo loti tizilalikirako kufupi ndi nyumba yathu ndipo zimenezi zingatithandize kuchepetsa mtunda woti tiziyenda popita kokalalikira.
4. Kodi chingatithandize n’chiyani kuti zinthu zizitiyendera bwino monga “asodzi a anthu”?
4 Yesu anafanizira anthu ogwira ntchito yolalikira ndi “asodzi a anthu.” (Maliko 1:17) Cholinga cha msodzi sichikhala kungoponya ukonde m’madzi koma kupha nsomba. Choncho, asodzi amene zinthu zimawayendera bwino amapita kumalo amene angapeze nsomba ndiponso pa nthawi imene angaphe nsombazo. Akafika kumalowo amayamba kupha nsomba nthawi yomweyo. Iwo amachita zimenezi mwanzeru kwambiri. Tiyenitu nafenso tizichita khama pa ntchito yolalikira.—Aheb. 6:11.