Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • Genesis 35:23
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 23 Ana aamuna amene Leya anaberekera Yakobo anali Rubeni+ mwana wake woyamba, Simiyoni, Levi, Yuda, Isakara ndi Zebuloni.

  • Genesis 37:26
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 26 Yuda atawaona, anauza abale ake kuti: “Tipindulapo chiyani tikapha m’bale wathu ndi kubisa imfa yake?+

  • Genesis 38:15
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 15 Yuda ataona mkaziyo, anaganiza kuti ndi hule+ chifukwa anali ataphimba nkhope yake.+

  • Genesis 44:18
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 18 Tsopano Yuda anayandikira kwa Yosefe n’kunena kuti: “Chonde mbuyanga, ndapota nanu. Lolani kuti kapolo wanune ndinene mawu amodzi okha.+ Chonde musandipsere mtima,+ pakuti inu muli ngati Farao+ yemwe.

  • Genesis 49:8
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 8 “Koma iwe Yuda,+ abale ako adzakutamanda.+ Dzanja lako lidzakhala pambuyo pa khosi la adani ako.+ Ana a bambo ako adzakugwadira.+

  • 1 Mbiri 2:3
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 3 Ana a Yuda anali Ere,+ Onani,+ ndi Shela.+ Mwana wamkazi wa Sua Mkanani ndiye anam’berekera ana atatuwa. Ere mwana woyamba wa Yuda anachita zoipa pamaso pa Yehova, ndipo iye anamupha.+

  • Chivumbulutso 5:5
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 5 Koma mmodzi wa akulu aja anandiuza kuti: “Tonthola. Taona! Mkango wa fuko la Yuda,+ muzu+ wa Davide,+ anapambana pa nkhondo+ moti iye ndiye woyenera kumatula zidindo 7 zimene amatira mpukutuwo ndi kuutsegula.”

  • Chivumbulutso 7:5
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 5 Mu fuko la Yuda,+ anadindamo anthu 12,000.

      Mu fuko la Rubeni,+ 12,000.

      Mu fuko la Gadi,+ 12,000.

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena