16 “Inu Yehova wa makamu, Mulungu wa Isiraeli+ wokhala pa akerubi, inu nokha ndinu Mulungu woona wa maufumu onse a padziko lapansi.+ Inuyo munapanga kumwamba ndi dziko lapansi.+
4 Tsopano ulemerero wa Yehova+ unachoka pa akerubi n’kupita pakhomo la nyumba yopatulika, ndipo mtambo+ unadzaza nyumbayo pang’onopang’ono. Komanso ulemerero wowala wa Yehova unadzaza m’bwalo lonse la nyumbayo.