Ekisodo 5:2 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 2 Koma Farao anati: “Yehova ndani+ kuti ndimvere mawu ake, ndi kulola Aisiraeli kuti apite?+ Ine sindikum’dziwa Yehova ngakhale pang’ono,+ komanso, sindilola kuti Aisiraeli apite.”+ Ekisodo 7:4 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 4 Komabe Farao sadzakumverani,+ motero ndidzaonetsa mphamvu ya dzanja langa pa Iguputo ndi kutulutsa makamu anga,+ anthu anga,+ ana a Isiraeli,+ m’dziko la Iguputo ndi ziweruzo zamphamvu.+ Ekisodo 14:8 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 8 Choncho Yehova analola Farao mfumu ya Iguputo kuumitsa mtima wake,+ ndipo anathamangira ana a Isiraeli pamene iwo anali kutuluka ndi dzanja lokwezeka.*+ Aroma 9:17 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 17 Pakuti ponena za Farao, Lemba linati: “Ndakusiya ndi moyo kuti ndikusonyeze mphamvu zanga, ndi kuti dzina langa lilengezedwe padziko lonse lapansi.”+
2 Koma Farao anati: “Yehova ndani+ kuti ndimvere mawu ake, ndi kulola Aisiraeli kuti apite?+ Ine sindikum’dziwa Yehova ngakhale pang’ono,+ komanso, sindilola kuti Aisiraeli apite.”+
4 Komabe Farao sadzakumverani,+ motero ndidzaonetsa mphamvu ya dzanja langa pa Iguputo ndi kutulutsa makamu anga,+ anthu anga,+ ana a Isiraeli,+ m’dziko la Iguputo ndi ziweruzo zamphamvu.+
8 Choncho Yehova analola Farao mfumu ya Iguputo kuumitsa mtima wake,+ ndipo anathamangira ana a Isiraeli pamene iwo anali kutuluka ndi dzanja lokwezeka.*+
17 Pakuti ponena za Farao, Lemba linati: “Ndakusiya ndi moyo kuti ndikusonyeze mphamvu zanga, ndi kuti dzina langa lilengezedwe padziko lonse lapansi.”+