Ekisodo 7:11 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 11 Komabe, Farao nayenso anaitana amuna ake anzeru ndi amatsenga.+ Choncho ansembe ochita zamatsenga a ku Iguputo anachitanso zomwezo mwa matsenga awo.+ Ekisodo 8:7 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 7 Komabe, ansembe ochita zamatsenga anachitanso zomwezo mwa matsenga awo, ndipo anachititsa achule kubwera pamtunda m’dziko la Iguputo.+ Danieli 1:20 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 20 Pa nkhani iliyonse imene mfumu inali kufunsira nzeru kwa iwo kuti imvetse bwino,+ inaona kuti iwo anali anzeru kuwirikiza maulendo 10 kuposa ansembe onse ochita zamatsenga+ ndi anthu onse olankhula ndi mizimu+ amene anali mu ufumu wake. Machitidwe 8:9 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 9 Tsopano mumzindawo munalinso munthu wina dzina lake Simoni. Izi zisanachitike, iyeyu anali kuchita zamatsenga+ ndi kudabwitsa anthu onse mu Samariya. Anali kudzitamandira kuti anali wopambana.+ 2 Akorinto 11:14 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 14 Ndipo zimenezo n’zosadabwitsa, popeza ngakhale Satana amadzisandutsa mngelo wa kuwala.+ 2 Timoteyo 3:8 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 8 Tsopano monga mmene Yane ndi Yambure+ anatsutsira Mose, anthu amenewanso akupitiriza kutsutsa choonadi.+ Iwo ali ndi maganizo opotoka kwambiri,+ ndipo sakuyenerera chikhulupirirochi.+
11 Komabe, Farao nayenso anaitana amuna ake anzeru ndi amatsenga.+ Choncho ansembe ochita zamatsenga a ku Iguputo anachitanso zomwezo mwa matsenga awo.+
7 Komabe, ansembe ochita zamatsenga anachitanso zomwezo mwa matsenga awo, ndipo anachititsa achule kubwera pamtunda m’dziko la Iguputo.+
20 Pa nkhani iliyonse imene mfumu inali kufunsira nzeru kwa iwo kuti imvetse bwino,+ inaona kuti iwo anali anzeru kuwirikiza maulendo 10 kuposa ansembe onse ochita zamatsenga+ ndi anthu onse olankhula ndi mizimu+ amene anali mu ufumu wake.
9 Tsopano mumzindawo munalinso munthu wina dzina lake Simoni. Izi zisanachitike, iyeyu anali kuchita zamatsenga+ ndi kudabwitsa anthu onse mu Samariya. Anali kudzitamandira kuti anali wopambana.+
8 Tsopano monga mmene Yane ndi Yambure+ anatsutsira Mose, anthu amenewanso akupitiriza kutsutsa choonadi.+ Iwo ali ndi maganizo opotoka kwambiri,+ ndipo sakuyenerera chikhulupirirochi.+